Chichewa

Emmanuel Ngwira: Katswiri wa vimbuza

Listen to this article

Gule wa vimbuza si wachilendo kwa Amalawi ambiri. Takhala tikuona guleyu akuvinidwa m’mawailesi akanema osiyanasiyana. Lachinayi lapitali mtolankhani wathu Martha Chirambo adacheza ndi katswiri wa guleyu Emmanuel Ngwira yemwe amavina vimbuza. Ngwira ndi mtsogoleri wagulu lovina la Kukaya lomwe lidayamba m’chaka cha 2005. Kucheza kwawo kudali motere:

Ngwira: Ndimadzichepetsa

Kodi Emmanuel Mlonga Ngwira ndi ndani?
Ndine mzibambo wa zaka 43. Ndili pa panja ndi ana atatu. Mkazi wanga ndi namwino pa chipatala cha Rumphi. Ndimachokera m’mudzi mwa Zinyongo Makwakwa, T/A Mpherembe m’boma la Mzimba. Timakui ku Elunyeni.  Uku nkomwe ndakulira, kuphatikizirapo ku Chikwawa ndi mzinda wa Mzuzu. Moti sukulu yanga ya sekondale ndidaphunzira pa sukulu ya Katoto ndipo kuchoka apo ndakhala ndikuchita maphunziro osiyana osiyana okhudza za maimbidwezi. Ndine mkhirisitu wa mpingo wa Katolika.
Ndili ndi certificate yochokera ku sukulu ya ukachenjede ya Pretoria koma ndinkaphunzilira konkuno ku Centre for Indigenous Instrumental for African Dance Practices. Ndidachita  maphunzirowa kwa zaka ziwiri.
Kupatula apo ndilinso ndi certificate mu zoimbaimba yochokera ku Chancellor College.
M’banja la mai wanga ndidabadwa ndekha pamene powerengera ku banja lina ndingati tilipo anthu asanu.
Udayamba bwanji kuvina vimbuza?
Izitu nza m’magazi. Zidachokera ku makolo chifukwa choti mai anga adali a Vimbuza. Iwo sankavina ayi; koma adali ngati asing’anga chifukwa ankalota ndipo munthu wolotedwayo amabweradi kudzafuna mankhwala kwa iwowo mpaka kuchira.
Nanga udayamba liti?
Ndidayamba kuvinaku m’chaka cha 1995 pomwe wansembe wina wampingo wa katolika Reverend Alex B Chima yemwe adali ndi gulu lake la Kukwithu Troop patchalitchi ya St Peters mu Mzuzu Diocese.
Atandiona kuti ndili ndi maluso osiyanasiyana, adanditenga dziko lonse la Malawi kuchita kafukufuku wa zomwe zimachitika kuti munthu azivina. Adatifunsa ngati wina mwa ife ali ndi gule woti gulu lathu lingamavine, ndidayambitsa guleyu ndipo ndidaphunzitsa anthu nyimbo.
Kuchokera nthawi imeneyo ndidayambapo kupititsa patsogolo luso langa.
Kodi muli ndi vimbuza kapena?
Ayi ndithu. Ine ndimangovinapo ngati gule basi. Ndilibe vimbuza ndine wabwinobwino ndithu ndilibe mizimu yoipa. Ngakhale mutapita kumalo osungirako zinthu zakale zopatsa chidwi a Mzuzu Museum, mukapeza kuti kuli zithunzi zanga zomwe adajambula nditapambana pampikisano womwe udachitika ku Rumphi. Ndidapikisana ndi asing’anga 34.
Kodi n’chifukwa chani mumavina guleyu?
Pali zifukwa zinayi zomwe ndimavinira guleyu monga: Kusangalatsa anthu, kuwaphunzitsa zosiyanasiyana kudzera m’magule, kusunga chikhalidwe komanso kupititsa patsogolo chikhalidwe.
Kodi anthu amati chani za inu.
Kuchokera kubanja langa, ndakhala ndikunenedwa kuti bwanji ndimavina magule osiyanasiyana. Anthu amandiyankhula zambiri zosiyanasiyana ndipo amanditenga ngati sindimadziwa zomwe ndikuchita koma ineyo ndimakhulupilira kwambiri mizimu. Mayi ndi bambo anga adamwalira kalekale komabe ndimakhulupilira kuti mizimu yawo imanditeteza. Ichi ndi china mwachifukwa chomwe ndimavina modzipereka kwambiri ndipo anthu amandipatsa ndalama zambiri.
Mumavinanso magule anji?
Mwa ena ndimavina mganda, malipenga ndi chilimika zochokera ku Nkhata Bay, mapenenga a ku Karonga, beni kuchokera ku Mangochi komanso mwinoghe a ku Chitipa.
Nanga okunenaniwa mumathana nawo bwanji?
Ndine wodzichepetsa. Ngakhale amandinena, sakudziwa zabwino zomwe ndimapeza kudzera mukuvinaku. Pakadalipano ndine mtsogoleri wa bungwe la Malawi Folk Dance Music and Song Society. Ndimapeza zosowa zanga zonse kudzera nkuvinaku. n

Related Articles

Back to top button
Translate »