Kuchoka kwa Phoya kutisokoneza, atero ena

Anthu m’madera osiyanasiyana m’sabatayi ati kuchoka kwa phungu wa chipani cholamula cha DPP m’dera la ku m’mawa m’boma la Blantyre, Henry Phoya kwasiya mafunso ambiri m’mitu yawo zomwe ati zingawasokoneze podzavota m’chaka cha 2014.

Anthuwa ati kuchokako kukusonyeza kuti kuchipani cholamula kwavunda zomwe ati zawachititsa kakasi kuti aone komwe angadzaponye voti yawo.

Koma katswiri wa za mbiri ya kale, Chijere Chirwa wati andale amachokachoka m’zipani zawo kapena kuyambitsa chipani chawo kotero izi sizikuyenera kusokoneza anthu.

Iye adati kuchoka kwa Phoya ukhale mwayi wa chipani cha DPP kuti apeze anthu ena atsopano omwe angamange chipanicho.

Phoya Lachiwiri adalengeza kuti walowa chipani cha MCP. Iye adalengeza izi pa msonkhano wa atolankhani omwe udachitikira kunyumba ya mtsogoleri wa chipanichi, John Tembo.

Pomwe Phoya amalengeza nkhaniyi, wachiwiri kwa mneneri wa chipani cha UDF, Ken Msonda adalengeza kuti wasiya ndale ndipo akukalera ana.

Mmodzi mwa anthuwo, Florence Kamvamtope wa m’mudzi mwa Kanyumbaaka kwa T/A Nsamala m’boma la Balaka wati kuchoka kwa Phoya kupita kuMCP kukulozera kuti pena pake paola ku DPP polingalira kuti Phoya adali msalamangwe kuchipaniko.

“Sitinganene kuti kupita ku MCP kungabweretse chitukuko. Izi zingotisokoneza mavotedwe chifukwa tikusowa chipani chomwe tingachione ngati chithandiza,” adatero Kamvamtope.

Ndipo Frank Chibambo wa m’mudzi mwa Chibwana kwa T/A Chikulamayembe m’boma la Rumphi adati izi zikuonetsa kuti ku DPP kwaipa.

“Apa pakuoneka kuti pali chikaiko kuchipani cholamula zoti iwo amalimbikitsadi ufulu wa demokalase. Zikundipatsa nkhawa kuti kodi zikhala zolongosoka?” sakukhulupirira Chibambo.

Koma Chirwa akuti munthu akatuluka chipani, chipanicho chikuyenera kutengerapo mwayi, pounguza ndi kupeza anthu omwe angapititse patsogolo chipanicho.

“Phoya adachotsedwa kuchipani cholamula ndiye ali ndi ufulu kupita kuchipani chilichonse nthawi yomwe adatsutsana ndi lamulo loletsa kutengera chiletso boma ndi ogwira ntchito m’boma.

“Tikatengera demokalase padalibe cholakwika chifukwa ngakhale uli kuchipani cholamula utha kumaperekerabe maganizo osemphana ndi ena,” adatero Chirwa.

Koma poyankhapo, Phoya wati anthu asadandaule chifukwa adziwa zoona zake posakhalitsapa.

“Sitikuvota mawa, ndiye tikhala tikulankhula ndi anthuwa kuti adziwe zingapo. Ndigwira ntchito yomwe akufuna.

“Ngati boma lingabwere ndi mabilu ena omwe sakomera Amalawi tiona kuti tithana nawo bwanji. Aboma akabweretsa zokomera anthu tiwathandiza koma ngati zikhale zosakomera anthu ndiye zioneka,” adatero.

Phoya adali phungu kuchipani cha UDF mu 1999 mpaka 2004 ndipo adakhalapo nduna muulamulirowo.

Iye adalowa hipani cha DPP ndipo adakhalaponso nduna muulamuliro wa chipanicho.

Share This Post