Maliro pa chisangalalo

Mwambo wa chikondwerero choti dziko lino latha zaka 53 lili pa ufulu wodzilamurira lidasanduka chisoni pomwe ana 7 ndi bambo mmodzi adamwalira pokanganirana kulowa m’bwalo la za masewero la Bingu National Stadium kumene kumayenera kuchitika mpira waulere.

Izi zidadziwika pomwe mtsogoleri wa dziko lino adatsogolera Amalawi pa mapemphero wolingalira za ufuluwo ku Bingu International Convention Centre (BICC) pomwe woyendetsa mwambowo mbusa Timothy Nyasulu adalengeza za omwalirawo. Iye adapempha anthu kuti akhale chete kwa mphindi imodzi polemekeza mizimu ya omwalirawo.

Wapolisi kuthandiza mmodzi mwa ana ku BNS

Ndipo nduna ya zamalonda ndi mafakitale Joseph Mwanamvekha, yemwenso adali wapampando wa komiti yoyendetsa mwambowo, adatsimikiza za imfa ya anthuwo mapemphero ali mkati. Iye adati anthu oposa 40 adavulala pangoziyo. Nthambi yofalitsa nkhani za boma lidati anthu 65 adamwalira.

Mutharika ndi mayi Gertrude Mutharika adakazonda anthu amene adavulala pa chipwilikiticho ku Kamuzu Central Hospital.

Mutharika adati :”Boma ndi lokonzeka kuthandiza pangoziyi.”

Dziko la Malawi limakumbukira kuti latha zaka 53 kuchokera pamene mtsogoleri wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda adakwanitsa kupeza ufulu kuchokera kwa Angerezi amene adayamba kulamulira dziko lino m’zaka za m’ma 1890. John Chilembwe, mmodzi mwa Amalawi oyambirira kufuna kumenyera ufuluwo adamwalira mu 1915.

Zikondwerero za chaka chino zinalipo kuyambira Lachitatu pa 5 July pomwe asilikali ndi achitetezo ena adayenda m’mizinda ya Blantyre, Zomba ndi Mzuzu.

Ndipo chikondwerero chimayenera kufika pa mponda chimera pa masewero a Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers amene amayembekezeka kuchitika kumalo a ngoziyo.

Komatu galimoto za chipatala ndi zapolisi zidali kukangalika kuthandiza ovulala pa zisawawazo.

Koma polankhula ndi Tamvani zisangalalozo zisanachitike, Amalawi ena adati ngakhale dzikoli latha zaka 53 likudzilamulira maloto ena amene adalipo pomenyera ufulu wa dziko lino.

Yemwe adakhalapo sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sam Mpasu adati m’Malawi wa zaka 53 ali panayi: Zina zasintha pang’ono, zina sizinasinthe, pomwe zina zaima kapena kubwerera mmbuyo.

Iye wati kunena mosapsatira zaka 53 sizidabweretse kusintha kwenikweni paulamuliro ndi kayendetsedwe ka maufulu a anthu m’dziko muno.

Mwa zina, iye adati ulamuliro wa Kamuzu Banda udayesera kubwezeretsa ulimi m’chimake pamene adakhazikitsa makampani otulutsa zinthu zina kunja zimene mu ulamuliro wa atsamunda zimakapangidwa kunja, koma zina sizikuyenda.

Adapereka zitsanzo za makampani a Sucoma, yomwe inkakonza shuga, Malawi Cotton yomwe inkaomba nsalu komanso British American Tobacco yomwe inkapanga ndudu ngati zina mwa zotsimikiza izi. Dziko lino lisanaladire ufulu, Mpasu adati zonsezi zinkabwera kuchokera kunja, ngakhale alimi ochuluka amene ankazilima m’dziko muno ankatumiza kunja chifukwa adali Atsamunda.

“Kamuzu  adayesetsanso kulimbikitsa msika wa mbewu kudzera ku Admarc ndipo adaonetsetsa kuti manyamulidwe a mbewu ngosavuta chifukwa kudali sitima za panjanji zomwe zimanyamula katundu pa mtengo otsika kupita ku misika,” watero Mpasu.

Ndipo mkulu wa bungwe loyang’anira za momwe maphunziro akuyendera m’dziko lino George Jobe wati pakutha pa zaka 53, Malawi amayenera kukhala ndi ntchito za umoyo za pamwamba motsatira chiyenerezo cha bungwe lalikulu loyang’anira zaumoyo la World Health Organisation (WHO) koma mmalo mwake zinthu zambiri sizikuyenda.

“Mpaka pano sitidayambe kukwaniritsa mlingo wa WHO oti K15 pa K100 iliyonse m’bajeti izikhala ya za umoyo. Chiwerengero cha ogwira ntchito za chipatala chikadali chotsika kwambiri poyerekeza ndi anthu omwe dokotala mmodzi amawona pa tsiku,” watero Jobe.

Ndipo kupatula zaumoyo, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zamaphunziro, Benedicto Kondowe wati sizoona kuti zaka 53 zingathe ana asukulu makamaka a kuma Yunivesite n’kumakhala pakhomo miyezi yambiri chifukwa cha mavuto m’sukulu zawo.

Iye wati pa zaka zonsezi, atsogoleri amayenera kukhala atapanga njira zothandizira kuti kalendala ya sukulu kuyambira ku pulayimale mpaka ku Yunivesite isamasokonekere chifukwa kutereku n’kulowetsa maphunziro pansi.

“Posachedwapa, aphunzitsi adali pa sitalaka pa nkhani ya maphunziro ndipo tikunena pano ophunzira m’ma Yunivesite sadatsegulire chitsekereni miyezi ingapo yapitayo nkhani yake kayendetsedwe,” adatero Kondowe.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.