Mzungu wolemba dikishonale ya Chichewa

 

Dikishonale kapena kuti buku lotanthauzira mawu ndi imathandiza anthu kupeza matanthauzo a mawu omwe akuwavuta kuti amvetsetse zomwe nkhani ikukamba. Nthawi zina pamakhala dikishonale yotanthauzira mawu a chilankhulo china kupita m’chilankhulo china. Mmodzi mwa anthu omwe dikishonale yotanthauzira Chichewa m’Chingerezi ndi mzungu wa ku Netherlands Steven Paas yemwe pano ali ndi zaka 74 zakubadwa ndipo wayenda ndi kuzungulira kwambiri pakati pa Achewa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Paas: Ndinkavutika pophunzira Chichewa

Ndiuzeni mbiri yanu.

Dzina langa lonse ndi Steven Paas ndipo ndidabadwa mu 1942 kwathu ku Netherlands. Ndimagwira ntchito za Mulungu imene ndidadzapezekera ku Malawi kuno.

Ndinu mzungu, ganizo lotanthauzira mawu a m’Chichewa lidabwera bwanji?

Chidwi chophunzira Chichewa chidakula kwambiri mmbuyomu. Pophunzira chilankhulochi ndinkakumana ndi zokhoma chifukwa kudali kovuta kumvetsetsa mawu ena. Ichi chidali chipsinjo chachikulu zedi moti zidandipangitsa kuyamba kulemba mawu ndi matanthauzo ake ndikawamva koyamba.

Mawuwa munkawamva kuti?

Monga ndanena kale, munthune ndine mtumuki wa Mulungu ndiye ndimakumana ndi anthu osiyanasiyana omwe amakhala ndi mawu osiyanasiyana. Kupatula apo, ndimakonda kuyenda m’madera kufufuza zomwe anthu amachita ndiye zina mwa zomwe zili m’bukhuli ndi zochitika m’madera makamaka ozungulira malo a Achewa omwe ndimacheza nawowo.

Sipangalephere mavuto, mudakumanapo ndi mavuto otani?

Monga mudziwa kuti nthawi zambiri anthu amakhala otchingira kwambiri makamaka pa zokhudza miyambo yawo kotero nthawi zina pofufuza, anthu ena amatha kuona ngati ndikuwafwala ndiye poteropo sizimayenda bwino mpakana ena omvetsetsa alowererepo  ndi kundithandiza.

Makamaka bukuli lidalembedwa motani?

Ndimalemba liwu la Chichewa n’kulitanthauzira

kenakonso lomwelo nkulilemba m’Chingerezi n’kulitanthauziranso kuti onse Achewa ndi Azungu apindule nalo komanso kwa ena, akhoza kuphunzira Chingerezi kapena Chichewa mosavuta poligwiritsa ntchito.

Zidakukomerani bwanji kukhazikitsa bukhu lolumikiza zilankhulo ziwiri?

Ndiyambira pa Malembo Oyera omwe amapezeka pa Genesesi 11 pomwe anthu adaganiza zomanga nsanja yokafika kumwamba ndipo Mulungu adawasokoneza ndi zilankhulo zosiyanasiyana kuti pulani yawo isatheke. Pamenepa pali phunziro lakuli ndipo n’kofunika ndithu kuti anthu ngakhale ali a zilankhulo zosiyanasiyana, pakhale njira yoti azimvana mosavuta. Mukadzalimvetsetsa buku, mudzaona kuti mposavuta munthu kumvetsetsa nkhani m’Chichewa kapena m’Chingerezi poligwiritsa ntchito. Apa ndiye kuti anthu azilankhulo ziwirizi athandizika.

Bukuli lidaunikidwa kale kuti lili bwino?

Zonse zidatheka kale ndipo lidasindikizidwa ndi a Oxford University Press ndipo likufalitsidwa ndi a Maneno Book Shop. Panopa tikungopemphera kuti a unduna wa zamaphunziro ayikepo chidwi ndi danga kuti ntchito imeneyi ipindulire ophunzira. n

Share This Post