‘Ulalo adali venda wa masiketi’

Makolo polangiza amati ukadekha, umawona maso a nkhono ndipo mwambi womwewu ansembe amati ukafuna kuvala kolona, ukuyenera kusunga khosi.

Miyambiyi siyapafupi kwa anthu ambiri kuyitsata koma umboni wake ulipo wa nkhaninkhani pakuti kwa iwo omwe adadekha n’kusunga makosi, pano

amadziwa momwe maso a nkhono alili ndipo kolona ali m’khosi.

Edward ndi Maggie tsiku la ukwati wawo

Apa pali umboni wa Edward Bannet Gangile wa kwa T/A Chiwere ku Dowa ndi Maggie Failo wa kwa T/A Malengachanzi ku Nkhotakota omwe ngakhale adakondana atangoonana koyamba, iwo adadekherana asadapalane ubwenzi.

Nthawiyo, m’chaka cha 2013, Gangile adali wowerengera za chuma ku chipatala cha mishoni cha Nkhoma ndipo akuti chipatalachi chimakonda kugula katundu monga mapepala ndi zolembera kushopu ya Maggie yomwe idali ku Area 3 mumzinda wa Lilongwe.

“Nthawiyo ndimayesetsa kumuthandiza mwachangu ndi mwansangala.

Timapatsana moni ndi kucheza nkhani zingapo koma ndimalephera kumuuza za kukhosi. Adandisangalatsa kwambiri ndi nsangala zomwe amandirandira nazo,” adatero Gangile.

Iye adati mpata udapezeka tsiku ali mushopumo ndipo mudabwera venda ogulitsa masiketi omwe adasangalatsa Maggie ndipo mwa izi, namwaliyo adamufunsa ngati angamugulireko mkazi wake.

“Ndimathokoza Mulungu kuti ndidaganiza msanga chifukwa ndidangoyankha kuti ndidzamugulira ndikadzamupeza ndipo yankholi lidamupangitsa kundifunsa mafunso ambiri pa zamoyo wanga kuphatikizapo kukayika kuti mwina ndimamunamiza,” adatero Gangile.

Iye adati ichi chidali chiyambi cha awiriwa kufufuzana ndikudziwana bwinobwino mpaka adavomerezana kuti onse amadikirana kutanthauza kuti aliyense mwa iwo adadekha kapena kusunga khosi.

Iye adati awiriwa adakhala miyezi ubwenzi usadayambe kwenikweni kuchoka panthawiyo ndipo zonse zitalongosoka, adapanga chinkhoswe pa 15 April, 2015 ku Area 47 kwa azakhali a Maggie ndipo ukwati udachitikira ku Lilongwe Golf Club pa 12 July, 2015.

Iye adati Maggie amamuuza nthawi ndi nthawi kuti ndi mwamuna wachikondi ndi olemekeza mkazi ndipo pachifukwachi, awiriwa akuti amakondana kwambiri moti adagwirizana zoyika chauta patsogolo mu chilichonse. n

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.