2018: Chaka cha ululu

Mu February 2018, Dorothy Kampani—Nyirenda amagwiritsira magetsi a K2 500 pa mwezi.

Kufika mu October mpaka lero, Nyirenda akugwiritsira magetsi a K5 000 pa mwezi.

Kukwera mtengo wa mafuta kudaliza Amalawi

Mayiyo amene amakhala ku Bangwe mumzinda wa Blantyre, adati mu February, 2018 amagwiritsira ntchito K700 kulipirira minibasi kuti akafike ku Trade Fair komwe amapanga bizinesi. Lero zasintha pamene akugwiritsira K1 000 mtunda womwewo.

Uwu ndiye ululu umene anthu akhala akuumva m’chaka cha 2018 kutsatira kukwera mtengo kwa mafuta agalimoto komanso kukwera kwa magetsi komwe kudapangitsa kuti zinthu zikwerenso.

Malinga ndi malipoti a Centre for Social Concern (CfSC), banja la anthu 6 m’chaka cha 2017, limafunikira likhale ndi K183 000 pa mwezi.

Izi zimachitika pamene ndalama yotsikitsitsa yomwe munthu amalandira idali pa K19 000.

Koma mu 2018, banja la anthu 6 limayenera likhale ndi K190 549 pa mwezi pamene ndalama yotsikitsitsa yomwe munthu amalandira idali pa K25 000.

Kutanthauza kuti banja la anthu 6 okhala m’tauni amalowa m’masautso osaneneka kuti athe mwezi umodzi chifukwa zomwe amapeza zimasiyana ndi zomwe zimafunikira.

Magetsi akhale akukwera m’chakachi. Pamene timamaliza 2017 n’kuti mafuta a petulo akugulitsidwa K888 00 pa lita imodzi ndipo dizilo adali pa K890 90 pa lita imodzi.

Mafutawo adakwera kanayi m’chakachi ndipo petulo adafika pa K990 50 pamene dizilo adafika pa K990 40 pa lita.

Izi zidachititsa kuti maulendo a minibasi akwere ndi 5 pelesenti m’dziko muno.

Mu October, bungwe logulitsa magetsi la ESCOM lidakweza magetsi ndi ndi 31.8 pelesenti. Kwa amene amagwiritsira magetsi a K7 714 pa mwezi adayamba kugwiritsira ntchito K10 105 pa mwezi.

Zinthu zambiri zofunikira pamoyo wa munthu zidakwera mtengo monga thumba la chimanga lolemera ndi makilogalamu 50 lidafika pa K10 000 kuchoka pa K5 000 mu June m’chakacho.

Kwa Kampani—Nyirenda, chakachi chidali chowawa chifukwa mitengo ya zinthu zidakhazikike.

“Vuto lalikulunso n’kuti bizinesi simayenda ndiye kuti upeze ndalama yogulira chakudya pakhomo ndi yoyendera kwakhala kovuta,” adatero.

Mkulu wa bungwe loona za anthu ogula la Consumer Association of Malawi (Cama), John Kapito adati ngakhale m’chakachi ndalama ya kwacha idaoneka kuti idali ndi mphamvu, komebe izi sizidathandize ogula.

“Anthu akuvutika kuti agule katundu, nthawi iliyonse mitengo ikungosintha. Boma likuyenera libweretse yankho kuti chaka chino anthu asavutike,” adatero.

Kapito adati chaka cha 2019 chingakhale chabwino kwa anthu ngati boma litaonetsetsa kuti mitengo ya zinthu zofunikira kwambiri pamoyo wa munthu sizikukwera mwachisawawa.

Share This Post