Nkhani

Alipa nkhuku 70 atatayira chimbudzi pachitsime

Listen to this article

Gulupu Chinyamula kwa T/A Kamenyagwaza m’boma la Dedza walipitsa amayi awiri nkhuku 35 aliyense chifukwa chotaira chimbudzi pachitsime.

Iye walamulanso kuti nyakwawa Chinyamula alipe nkhuku ziwiri chifukwa milanduyi idagwa m’mudzi mwake.Chicken_farming

Gulupu Chinyamula adati sabata yatha, mjigo wa m’mudzi mwawo udaonongeka ndipo akulephera kukonza.

Malinga ndi gulupuyu, anthu 1 500 a m’midzi 10 imene ili pansi pake amamwa mjigo umodzi ngakhale akhala akudandaula kwa a mabungwe kuti awakumbire wina. Kaamba ka kuchuluka kwa anthu ogwiritsira ntchito mjigowu, sikuchedwa kuonongeka.

“Aka sikoyamba kuti mjigo uonongeke, wakhala ukuonongeka kuyambira chaka chatha. Pamene waonongeka, midzi yonse imakamwa pachitsime pamene achitira chipongwepo.

“Tsono ulendo uno, pamene anthu anapita kukatunga pachitsimecho, adadabwa kuti munthu wachitiramo chimbudzi. Koma amene adapita mmawa, ataona zofiira m’madzimo, amangoti ndi masamba ndipo adatunga ndi kukagwiritsira ntchito madziwo,” adatero gulupuyu.

Iye adati anthu amene adabwera pachitsimepo dzuwa litatuluka ndiwo adazindikira kuti pachitsimepo wina wachitira chimbudzi.

Nyakwawa Chinyamula adati anthuwo adamuitanitsa kuchitsimeko ndipo idadzionera yokha kuti idali ndowe ya munthu. Kodi adaidziwa bwanji?

“Ine ndisadziwe chimbudzi cha munthu? Amene adatungawo adandionetsa ndipo ndidatsimikiza chifukwa pa nthawiyo nkuti isadasungunuke,” idatero nyakwawayo.

Nkhaniyo itapita kwa gulupu Chinyamula, iye akuti adaopseza kuti ayenda ndi chimbudzicho kwa ng’anga kuti amene wachitayo aone mbonaona.

“Tsiku lomwelo padabwera amayi awiri amene adati ndiwo adachita zimenezo. Sadafotokoze bwino chifukwa chomwe achitira izi koma adavomera pamaso panga kuti adakataya chimbudzicho ndiwo,” adatero gulupuyu.

Gulupu Chinyamula wati amaiwo adauza bwalo lake kuti adachita chipongwecho ngati njira imodzi yoti akuluakuku akonze mjigowo mwachangu.

Nkhaniyi itapita kubwalo, gulupuyo adagamula kuti mayi aliyense alipe nkhuku 35. Mayi mmodzi wapereka kale nkhukuzo pamene wina wangopereka nkhuku 15.

“Ndalandira nkhuku 35 kwa mayi mmodzi komanso nkhuku 15 ndipo kwatsala nkhuku 20,” adatero gulupuyu.

Iye wati bwalo lake limaloledwa kulipitsa nkhuku. “Ndine gulupu, nkhani ikafika pabwalo langa, ndimalipitsa nkhuku basi. Bwalo la T/A limalipitsa mbuzi pamene kubwalo la paramount kumagwa ng’ombe,” adatero pamene olakwawo sadapatsidwe mwayi wolipira ndalama akalephera kulipa nkhuku.

“Nkhukuzi tigulitsa ndipo ndalama yake tikonzetsera mjigowu, mafumu anga ndawauza kale za nkhaniyi ndipo ntchito yokonza mjigowu iyamba sabata ikudzayi,” adatero.

Nyakwawa Chinyamula wati anthu asiya kugwiritsira chitsimecho ndipo akumba zitsime zina kumadimba komwe akulima mizimbe.

“Tidaitanitsa wa zaumoyo kuti adzathire mankhwala pachitsimepo koma mpaka pano sadabwere, chomwe tapanga ndikukumbanso zitsime zina kumadimba komwe tikumwa pano,” idatero nyakwawayi.

Amai awiriwo adakana kulankhula ndik mtolankhani wathu za nkhaniyi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »