‘Kudali ku Spar ya ku City Centre’
Beatrice Mushani adakayamba ntchito ku Spar ya ku City Centre mu mzinda wa Lilongwe pa 1 October, 2018. Ndipo udali m’mawa wa tsikulo pomwe adakumana ndi Noel Kajani koyamba panja pa shopuyo, apa n’kuti akudikira kuti malowa atsegulidwe.
Panthawiyo n’kuti Kajani akugwira kale ntchito ku Spar konko.
Pang’onopang’ono awiriwo adayamba kucheza maka pomwe Mushani ankamufunsa Kujani kuti ntchito ya mu Spar imakhala bwanji.
“Pamene timadikira kuti titsegule shopu, ndi pomwe ndidamuonera Beatrice ndipo ndidali woyamba kuyankhula naye pomwe amadzayamba ntchito,” adalongosola Kajani.
Iye adati adakopeka ndi Mushani tsiku lomwelo ndipo patadutsa miyezi itatu adamufunsira.
Patadutsa chaka ndi miyezi 7 ali pa ubwenzi, awiriwo adakwatirana pamwambo wopambana omwe udachitikira ku Lewis Garden, mumzinda
wa Lilongwe pa 4 July 2020.
Iwo adati akakumana ndi mavuto amakhala pansi ndi kukambirana komanso amamupempha Mulungu kuti aziwathandizira.
Padakalipano Kajani akugwira ntchito kukampani ya Seed Co Malawi Limited pomwe Mushani amagwira ntchito ku Spar ya ku City Centre mumzinda wa Lilongwe.
Kajani amachokera m’mudzi mwa Gonthako, ka T/A Mabulabo, m’boma la Mzimba pomwe Mushani amachokera m’mudzi mwa Kadole, T/A Mwabulambia, m’boma la Chitipa. Koma iwowa akukhalira ku Area 12, mumzinda wa Lilongwe.