Nkhani

‘Chuma chifike kumudzi’

Nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha ati ndondomeko ya za chuma imene apereka m’Nyumba ya  Malamulo dzulo ikuonetsetsa kuti chuma chochoka ku thumba la boma chizifikadi kwa Amalawi akumudzi.

Boma likuyembekezera kugwiritsa ntchito K10.978 triliyoni kuyambira chaka chino mpaka chaka cha mawa.

A Mwanamvekha (Kumanja) kufika ku Nyumba ya Malamulo dzulo. | Jacob Nankhonya

M’bajetiyo, a Mwanamvekha adati boma lachilimika poika ndalama zochuluka ku za ulimi, zikopa alendo, za migodi ndi mafakitale.

Ku nkhani ya za ulimi kulowa K931 biliyoni pomwe zokopa alendo ndi mafakitale kupita K51.2 biliyoni pomwe za mphamvu ndi migodi kulowa K352 biliyoni.

Pa nkhani ya maphunziro, boma ligwiritsa ntchito K1.28 triliyoni, pomwe za umoyo kulowa K1.02 triliyoni. Nkhani ya za mtengatenga ndi mtokoma kulowa K664.3 biliyoni.

Ku thumba la chitukuko la CDF kulowa K1.45 triliyoni.

Polankhula ndi atolankhani atapereka ndondomeko ya momwe boma ligwiritsire ntchito chuma chake chaka chino mpaka chaka cha mawa, a Mwanamvekha anati bajetiyo aikonza moti chuma chiyambenso kuyenda bwino. Iwo anati chachikulu n’choti Amalawi nawo azitha kuchita mapulani pa momwe zikuyendera pa nkhani ya chuma pakhomo.

“Tikufuna kukonza chuma chathu kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino. Komanso tikufuna Amalawi ayambe kupanga pulani chifukwa kayendetsedwe ka chuma kakhazikika. Tionetsetsanso kuti ndalama zichoke ku thumba la boma ku Lilongwe zipite kumudzi komwe zikagwire ntchito ya chitukuko,” atero a Mwanamvekha.

Iwo adati izi zikusiyana ndi mmbuyomu pomwe ‘ndalama zimangopita ndi kumangodyedwa, osati kugwiritsa ntchito njira zosakhala za chitukuko’.

“Komanso taonetsetsa kuti makampani amene akupanga zinthu m’Malawi muno tiwateteze kuti azitha kupanga zinthuzo mosavuta. Tikufuna kulimbikitsa kuti tizitumiza zinthu kunja,” adatero a Mwanamvekha.

Ndipo adaonjeza kuti mitengo ya zinthu ikuyenera kukhala yokhazikika. Chiongola dzanja Amalawi akatenga ngongole chisakhale chokwera.

A Mwanamvekha adapereka bajeti ya K10.98 triliyoni ndi cholinga chachikulu choti ndalama zimene boma limapeza ndi zomwe limagwiritsa ntchito zisasiyane kwambiri. Bajetiyo ikuyesetsanso kuti boma lizitolera ndalama zochuluka komanso kuyesetsa kuti boma libwenze ngongole zimene lili nazo.

Koma mkulu wa zipani zotsutsa boma a Simplex Chithyola Banda adati bajeti imene apereka a Mwanamvekha siikupereka chiyembekezo kwa Amalawi makamaka chifukwa misonkho yankitsa.

Polankhula ndi mtolankhani wathu, a Chithyola Banda adati misonkho yachuluka moti ogwira ntchito m’boma akupita n’kochepa ku nyumba.

“Amalawi akulira ndi misonkho imene amadulidwa ku malipiro awo a pa mwezi. Timaona ngati boma lisintha izi, koma ayi ndithu, kuli chuuu! Kutsutsula chilondacho, akuonjezeranso misonkho ina. Kodi ng’ombe imene mukuidyetsa mosakwanira, kuti muikame, mupeza mkaka kapena magazi?” adazizwa iwo.

Pa nkhani yoti mtengo wa chimanga ukhale wokhazikika, a Chithyola Banda adati boma limayenera kuunikira bwino pa zomwe alimi amaika kuti akolole chimanga.

“Tikuyenera kuunikira mbali zones, olima ndi ogula chimangacho. Ngati sitiunikira bwino kuti alimi amalowetsa zingati polima chimanga n’kumangoti chitsike mtengo, alimi ambiri agwa mphwayi. Mapeto ake ndi njala,” atero iwo.

Mkulu wa bungwe loona za maboma aang’ono ya Malawi Local Government Association (Malga) a Hadrod Mkandawire ati mawu awowa apherezera popeza K33.70 ya K100 iliyonse ayiika ku thumba la CDF komwe kwalowa K1.145 triliyoni.

“Izi zikupereka chithunzithunzi chabwino pa nkhani yoti boma likufuna kuti zimene likulankhula zizionekadi m’midzimo. Ndi chiyembekezo chathu kuti zomwe anena lero zikafikadi momwe aneneramo chifukwa mmbuyomu zakhala zili zosiyana,” adatero a Mkandawire.

Nthawi yomwe a Mwanamvekha amalankhula, aphungu amachilandira mosiyanasiyana. Akalankhula mokomera aphungu a mbali ya boma, aphungu a mbaliyo amakuwa kuti: “Boma ilo!”

Koma akalankhula zoti otsutsa sizinawakomere, amazuma, moti mpaka kangapo konse a Mwanamvekha adapempha sipikala wa nyumbayo a Sameer Suleiman kuti awateteze posungitsa bata.

“Chonde tiyeni tisunge bata. Aphungu ena mukuyendayenda, kusokoneza zochitika m’nyumbayi. Koma ndithokoze aphungu a zipani za UTM, UDF ndi ena amene muli pa maso panga kaamba kosunga bata,” adatero a Suleman m’nyumbayo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button