Nkhani

Amanga mayi pa mlandu wovulaza m’nzawo ku nkhope

A Police ku Neno amanga a Grace Samuel a zaka 33 kaamba kowaganizira kuti anavulaza mayi m’nzawo atamuthira madzi otentha ku nkhope pomuganizira kuti anali pa ubwenzi wamseli ndi mwamuna wawo.

Mneneli wa polisi ku Neno a Rebecca Msoliza anati oganizilidwawa akhala akukaikira kuti amuna awo anali pa ubwenzi wa mseli ndi mayi wina yemwenso ndi okwatiwa koma mwamuna wake ali m’dziko la South Africa.

Iwo anati pa July 5 2026, a Samuel adapeza mauthenga omwe mkazi m’nzawoyo anatumiza kudzera ku lamya ya mwamuna wawo zomwe zidawakwiyitsa ndipo anaganiza zoyitanira mkaziyo kunyumba kwawo kuti akakambirane pamodzi ndi mwamuna wawo.

A Msoliza anati mkazi m’nzawoyo sananyalanyaze ndipo adapitadi kunyumba kwa a Samuel kuti akakambirane, koma zokambilana zawo sizidathe bwino.

“Ali mkati mokambirana, oganizilidwawa anapsa mtima ndipo anatenga poto wa madzi otentha ndi kuthira mkazi m’nzawoyo ku nkhope,” anatero a Msoliza.

Iwo anati anthu achifundo adatengera mayi ovulazidwayo ku chipataka cha Nsambe asanamutumize ku chipatala chachikulu cha m’bomali kuti akalandire thandizo.

Pa July 8 2026, mayi wovulazidwayo anakatula nkhaniyi ku polisi zomwe zidachititsa kuti woganiziridwayo amangidwe.

Padakali pano, oganizilidwayo akadali m’chitokosi cha apolisi ndipo akaonekera ku bwalo la milandu posachedwa komwe akayankhe mlandu wovulaza munthu.

A Samuel amachokera m’mudzi mwa Kaingilira, mfumu Dambe m’boma la Neno.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button