Mayi wakakamira kuti mlandu wake uwerudzidwe, uthe
Mau aja amati kumayenda kuti uone agalu a michombo adapherezeka mkati mwa sabatayi pomwe mayi wina wa zaka 22 ku Ntcheu adaoneka ngati wodzimbuka ati pokakamira kuti mulandu wake ugamulidwe nthawi yomweyo pomwe iye adakaonekera ku bwalolo.
Mayiyo, a Lonjezo Divala a m’mudzi wa Chikonga kwa Chakhumbira m’bomalo, ulendo uno adaoneka mosiyana. Anali odekha ndipo sanali molankhula zambiri kusiyana ndi tsiku lomwe adadzaonekera koyamba ku bwalolo.

Apolisi ku Lizulu adamanga a Divala pa May 10 chaka chino powaganizira kuti adabaya ndi mpeni a Mike Smith omwe akuti amagayitsa m’chigayo china pa msika wa Lizulu. Izi akuti zidachitika pa malo ena ogona alendo a Kaboma. Akuti ovulazidwayo, yemwe amachokera m’muďzi mwa Sala kwa Ganya m’bomalo, adali pa ubwenzi ndi mayiyo.
Malingana ndi oyimira boma pa mulanduwo a Blessings Kajogolo, a Divala adabaya bambowo ataipidwa poona kuti adatengana ndi mayi wina a Jenita Maliyasi omwe nawonso ntchito yawo njoyendayenda pa msikapo. A Maliyasi amachokera m’mudzi mwa Mapira kwa Chakhumbira komweko.
A Maliyasi, omwe adagwiritsidwa ntchito ngati mboni yachiwiri ya boma pa mulanduwo, adati zonse zidayamba pomwe a Smith adatengana nawo n’kumakamenya masewera a Pool pamalopo uku akumwetsana mowa.
“Pa nthawiyo, nkuti awiriwo atayambana chifukwa sadalankhulitsane mwamtendere. Posakhalitsa, adafika pomwe tidalipo nkukokerana ku chipinda akusemphanabe maganizo. Mpomwenotu timadzamva kufuula. Izi zidachitikira mu Room 5 ya pamalowo ngakhale kuti m’nzangayo yake idali Room 4. Zidali zoopsa kuona momwe bamboyo adataira magazi kaamba ka balalo,” adatero a Maliyasi.
Pa tsiku lodzamva mulanduwo kwa nthawi yoyamba, a Divala adavomera kuti adachitadi za upanduzo, koma iwo adati adachita izi mosazindikira.
“Mutu wanga sunkagwira pomwe ndimachita izi. Pa tsikulo, ndidali ntaupapira mowa kotero kuti zambiri ndinazimvera pomwe adanditola apolisimu,” adatero mayiyo.
Chosadziwa chidali chakuti naye woweruza mulandu, a Pleasant Sichali atamva izi, adangoti pamenepo cholembera chake khwee, kuti apeza podzayambira ulendo wina.
Ndipo mkati mwa sabatamu, nkhaniyo idayambiradi pompo pomwe bwaloli limafuna kuti lipeze umboni kuti a Divala m’mutu mwawo simunkagwiradi ntchito pa tsikulo.
Apa mpamene iwo adauza bwalolo kuti sakufuna kunenanso kali konse pa mulanduwo ndipo mmalo mwake, oweruzayo angomugamula— chichitike-chichitike!
Ndipo ngakhale bwalo lidaperekabe mpata kuti mwina adziikirebe kumbuyo monga momwe malamulo amanenera, a Divala adamenyetsa nkhwangwa pa mwala kuti sakupanga nawo, m’maso muli gwaa!
Koma poona nthawi ikupita, bwalolo lidatsindikanso kuti zikatero, lamulo limati udindo woonetsa kuti palakwiridwa umakhala ndi obweretsa mulandu omwe ndi oyimira boma. Ndipo chifukwa chakuti woganiziridwa adakana kulankhulapo, bwaloro lidakonza chigamulo chake potengera zomwe aboma ndi mboni zawo adapereka.
Malingana ndi zowerengedwa mkati la bwaloli pa mulanduwo, a Divala adabaya ndi kuvulaza kwambiri mwamunayo pogwiritsa ntchito mpeni wa sikisi giya womwe udali wakuthwa kwambiri kotero kuti maliseche a wovulazidwawo adafika ku chipatala ali lendelende.
“Nde paja mudati simunkadziwa chomwe chinkachitika kaamba ka kuledzera ndiponso kuti simukudziwa kuti mudaledzera bwanji? Bwalo lino lakanikatu kupeza umboni kuti mwina mowayo anthu ankachita kukukamaizani kukamwa kwanu kuti mumwe, muledzere. Chimenecho mwina nchomwe chidakakupulumutsani,” adatero woweruza mulanduwo, zomwe zidadzetsa phwete kwa omvera onse.
Wolakwayo amayenera kukakhala ku ndende kwa zaka zosachepera 7, koma bwalolo lidachotserako miyezi 36 yoyambilirayo kaamba koti n’koyamba kupalamula.



