Sitima za tsopano zidzafewetsa miyoyo
Anthu okhala mozungulira, komanso pa zisumbu m’nyanja ya Malawi; pamodzi ndi ochita malonda osiyanasiyana akuyembekezera ndi chidwi kupherezera kwa lingaliro la boma lokhazikitsa sitima zinayi zatsopano pa nyanjayi.
Chiyembekezochi chikudza polingalira zipsinjo zomwe zakhala zilipo kwa nthawi yaitali monga kusadalirika, komanso chiopsezo cha ngozi pa maulendo a pa nyanja zomwe sitima zatsopanozo zikuyembekezeka kudzathetsa pambali pokweza ntchito za malonda makamaka ndi maiko oyandikana nawo.

Masiku apitawa, unduna woona za mtengatenga ndi mtokoma lidasainirana mgwirizano ndi kampani ya Xiao Xiang Investment ya ku China kuti ikonze sitima ziwiri zonyamula katundu, imodzi yonyamula mafuta ndi inanso yonyamula anthu; komanso kukonza madoko a Chipoka ku Salima ndi Kaporo m’boma la Karonga.
Ngakhale mbali ziwirizi sizidaulule ndalama zogwirira ntchitozi, mgwirizanowu ukutsimikizira chidwi chomwe chakhala chikusowa kumbali ya boma pa nkhani yokweza ntchito za mtengatenga makamaka wa pamadzi m’zaka zochuluka.
Kupatula kupumitsa sitima ya MV Ilala yomwe yakhala ikuyenda pa nyanja ya Malawi kwa zaka 75, ntchito yopanga sitima zatsopano ndi yokonza madoko awiriwo zidzachititsa nyanjayo kukhala mpita wodalirika pa nkhani za mtengatenga, komanso kuchepetsa mlingo wa katundu yemwe amayenda pa misewu ya m’dziko muno.
Mlembi wamkulu ku unduna woona za mtengatenga a Bright Kumwembe adati: “Mitengo ya maulendo, komanso yonyamulira katundu ikuyembekezeka kudzatsika sitima zinazo pamodzi ndi madoko awiriwo zikadzayamba kugwira ntchito. Tikuyembekezeranso kuti ntchito za mtengatenga, komanso malonda pakati pa dziko lino ndi oyandikana nawo zidzapitanso patsogolo.”
Malingana ndi a Kumwembe, imodzi mwa sitima zatsopanozo ikuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito m’miyezi 12 ikudzayi ndipo kupatula kuchepetsa kudalira kwambiri mayendedwe a pa msewu zidzachititsa kuti zokolola ndi katundu wina monga fetereza ndi mafuta a galimoto zizifika mosavuta m’dziko muno ngakhalenso kuzitumiza maiko ena.
Nyanja ya Malawi njotalika makilomita pafupifupi 580 ndipo phindu lokhazikitsa sitima za makonozo lidzafikira asodzi ndi alimi ochuluka kuyamba kutumiza nsomba ndi zokolola zawo m’madera ena akutali mosavuta. Nazo ntchito zokopa alendo ndi bizinezi zikuluzikulu zikuyembekezeka kudzapita patsogolo zedi.
“Tikuyembekezera kuti katundu monga zokolola zakumunda zizidzayenda mwa changu ndi motsika mtengo zomwe zidzachititsa kuti ndalama zochitira bizinesi pa msika zidzakhalenso zochepa,” adatero mtsogoleri wa bungwe la anthu ogula ndi kugulitsa mbeu m’dziko muno, a Grace Mijiga, popereka ndemanga yake.
“Tikukhulupilira kuti boma lidzakhazikitsanso malo abwino ndi odalirika osungira katundu ku madoko a Kaporo ndi Chipoka, komanso kuti katundu azidzakwezedwa ndi kutsitsidwa m’sitima mosavuta ndi motetezeka ngakhale atachuluka motani,” a Mijiga anaonjezera motero.
Madoko awiriwa ndi gawo lofunika kwambiri lolumikizitsa mayendedwe a pa nyanja, pa njanji ndi pa msewu, komanso kuteteza misewu yambiri yomwe yakhala ikuonongeka pafupipafupi kaamba konyamula katundu wochuluka mowirikiza.
Mtsogoleri wa gulu la eni kampani zothandizira kulowetsa katundu wa kunja m’dziko muno, a Yohane Kapalamula ati kukula kwa chiwerengero cha anthu ndi katundu oyenda pa sitima za pamadzi m’malo mwa pa galimoto kudzathandiza kutukula ntchito za mtengatenga m’dziko muno.
“Msewu wathu wa M1 udzapeputsidwa ndi kukhala wa ngwiro, komanso mtengo woitanitsira katundu monga mafuta a galimoto ndi zipangizo za ulimi udzatsikirapo. Kuonjezera apo, madera osiyanasiyana a mphepete mwa nyanja adzakhala olumikizika mosavuta,” adatero a Yohane.
Iwo adatsindika kuti kupambana kwa lingaliroli kwagona pokhala ndi madoko odalirika, misewu yabwino yolowera ndi kutuluka ku madokowo, kukonza ndi kusamalira sitimazo mowirikiza, komanso kupezeka kwa katundu woti azinyamulidwa pa sitimazo.
“Mayendedwe a pa madzi akuyenera kuthandizirana ndi a pa msewu osati kulowa m’malo mwake. Madoko amakono ndi ofunika kotero n’kofunika kuti adzakhala ndi malo aakulu oyendetsera ndi kusamutsira katundu mofulumira kuchoka pa nyanja kufika pa njanji kaya pa msewu. Madoko otere amachititsa kuti eni bizinesi azikhulupirira kwambiri mayendedwe a pa madzi,” adatero a Yohane.
Mneneri wa kampani ya Nocma a Raymond Likambale ati kukhazikitsa sitima yonyamula mafuta pa Nyanja ya Malawi kudzasintha kwambiri nkhani za mtengatenga m’dziko muno popereka njira yabwino, yotsika mtengo, komanso yodalirika yonyamulira mafuta ochuluka.
“Kusiyana ndi galimoto zonyamula mafuta, sitima izidzanyamula mafuta ochuluka pa kamodzi kupita nawo kumalo osungira m’mphepete mwa nyanjayi. Izi zidzachepetsa chiwerengero cha galimoto zikuluzikulu zonyamula mafuta m’misewu, komanso kuchepetsa ndalama zokonzera misewu,” adatero a Likambale.
Iwo adatinso dongosololi likufunika ndalama zochuluka zomangira ndi kukonzera madoko a makono, malo osungira mafuta, komanso kulimbikitsa ukadaulo wa chitetezo.
“Pakufunika kukhala ndi malo, komanso makina amakono otsitsira ndi kukwezera mafuta kumadoko, ukadaulo wosungira mafutawo, kugwiritsa ntchito njira za digito zochitira kalondolondo wa kayendedwe ka mafuta nthawi zonse, kuzindikira msanga kutaika kwa mafuta, komanso kuthandizira kuthana ndi ngozi zikachitika.
“Padzafunikanso njira za makono zoyendetsera sitima ndi zolumikizirana kuti kayendedwe ka mafuta pa nyanja ya Malawi kadzakhale kotetezeka, kodalirika, komanso kogwira ntchito bwino,” a Likambale adatero.
Mkulu wa kampani ya Xiao Xiang Investment a Chen Cheng adati: “Ntchito yomanga sitima zonyamula mafuta idzathandiza kwambiri kampani monga zoitanitsa mafuta a Nocma ndi Petroleum Importers Limited poonjezera mlingo wa mafuta onyamulidwa pakamodzi.”
A Cheng adatinso sitima zonyamula katundu zidzatsegula njira yolumikizira Malawi ndi madoko a Tanzania ndi Mozambique, kuchepetsa katundu pamseu wa M1, komanso kuonetsetsa kuti katundu akuyenda bwino makamaka m’nyengo yamvula pamene mayendedwe a pa msewu amasokonekera.



