Nkhani

Atuluka ku ndende pa milandu yogwiririra

Mabwalo akulu a milandu ku Zomba ndi Lilongwe apulumutsa anthu awiri omwe mabwalo a milandu a magistrate adawapeza olakwa pa milandu yogona ndi ana.

Mabwalowa apereka zigamulozi nthambi ya boma yoimira anthu milandu mwaulere itawaimira posakhutitsidwa ndi zigamulo za mabwalo ocheperakowo.

Iwo adagamula izi polingalira kuti a Maliko Nangwale a zaka 31 ku Zomba adali kwina nthawi yomwe amawaganizira kuti adagona ndi mtsikana wa zaka 14. Ndipo ku Lilongwe, mnyamata wina yemwe akungotchedwa CM amene adali ndi zaka 16 adapezeka wolakwa pomwe apolisi adamukakamiza kuti ali ndi zaka 22 nthawi yomwe adagona ndi mtsikana wa zaka 12.

Bwalo lalikulu ku Zomba lidalamula kuti Maliko Nangwale a zaka 31 atulutsidwe ku ndende komwe adagamulidwa kuti akakhale zaka 14 ndi bwalo la Zomba Magistrate pa mlandu wogwiririra mtsikana wa zaka 14, yemwe anali mwana wa eni nyumba imene amakhala m’chaka cha 2024.

Malinga ndi uthenga wa nthambiyo pa Facebook, CM adaonekera ku bwalo la magistrate ku Dedza pa 30 October chaka chatha pa mlandu womuganizira kuti adagona ndi mtsikana wosakwana zaka 18. Iye adauvomera mlanduwo ndipo bwalo lidagamula kuti akaseweze zaka 16 atauvomera mlanduwo.

“Koma mlandu utalowa m’bwalo la apilo pa 10 June chaka chino, woimira boma pa milandu a Edward Partridge adavomereza kuti ndi wachichepere. Ndipo womuimira kuchokera ku nthambiyi a Levison Seyani adagwirizana nawo,” idatero nthambiyo.

Ndipo pounikira mlanduwo, bwalo lidapeza kuti sitetimenti idaonetsa kuti poyamba adamulemba kuti ali ndi zaka 17 koma padasinthidwa kuti ali ndi zaka 22 popanda kufotokoza chimene chidachititsa kuti pakhale kukhwatchako. Zidatumphuka m’bwalolo kuti atamumanga, ndipo atanena kuti ali ndi zaka 17 apolisi adamuuza kuti avule ndipo poona kukula kwa katundu wake, adati ayenera kukhala ndi zaka 22.

“Poona izi, bwalo lidalamula kuti mnyamatayo akayezedwe ndipo adapita naye ku chipatala cha Kamuzu Central pa 20 August komwe adatsimikiza kuti adali ndi zaka 17,” idatero nthambiyo.

Potsatira izi, woimira boma adavomereza mfundo za nthambiyo kuti chigamulo cha bwalo loyamba chidali cholakwika

Apa bwalo lidagamula kuti mwanayo amutulutse pompopompo chifukwa mlandu wake umayenera kupita ku khoti la ana.

Ku Zomba, a Nangwale adapereka umboni woti patsiku lomwe amawaganizira kuti adagona ndi mwanayo adali akugwira ganyu ya zokhomakhoma ndi anzawo awiri omwe adaperekeranso umboni kuti adali ndi iwowo tsiku lonse ndipo sizinali zoona kuti adachita zomwe amamuganizirazo.

Koma woweruza adakana izi chifukwa sitetimenti ya polisi imene adasainira idasonyeza kuti adavomera mlanduwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button