Nkhani

Maneb ikhutila ndi mayeso a sitandade 8

Bungwe loyendetsa mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) lati lakhutira ndi mmene mayeso a Sitandade 8 ayambira.

Mkulu wa bungweli Roy Hauya adanena izi Lachinayi atayendera malo angapo komwe ophunzira amalembera mayeso kuyambira Lachitatu.

Lachitatu Hauya adayendera sukulu zina ku Blantyre ndipo Lachinayi adali ku Lilongwe.

“Takondwa ndi mmene mayeso ayambira. Nditsimikizire dziko lonse kuti mayeso akuyenda bwino. Anzathu achitetezo akugwira ntchito yawo bwino ndipo ophunzira akulemba momasuka.Tikufuna zipitirire chonchi Mmene tikhale tikuyamba mayeso ena mwezi ukubwerawu,”adatero Hauya.

Koma iye adavomereza kuti alandira lipoti lochokera m’boma la Mchinji loti munthu wina amalembera wophunzira wina mayeso.

“Pakadalipano tingati talandira mlandu umodzi wa mayesowa.Wolembera mnzake mayeso amugwira ku Mchinji,” adatero Hauya.

Ophunzira adamaliza mayeso awo dzulo Lachisanu.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button