Nkhani

Anthu a ku Likoma alirira Ilala

Listen to this article

Anthu okhala pazilumba za Likoma ndi Chizumulu ati akulira ndipo moyo ukutentha chifukwa cha kusiya kuyenda kwa sitima ya Ilala.

T/A Mkumpha wa ku Likoma yati kuleka kuyenda kwa sitimayo kwachititsa miyoyo ya anthu pa zilumbazo kukhala yovuta.

Malinga ndi iye, kuonongeka kwa sitimayo kwachititsa chiyembekezo chimene anthuwo adali nacho kwa miyezi 10 pomwe sitimayo imakozedwa kuti chilowe m’madzi akuya.

“Moyo ukuvuta pa Likoma chifukwa sitimayo si ikuyenda. Ntchito za chitukuko zaimiratu chifukwa cha vuto la mayendedwe,” adatero Mkumpha.

Sitimayo idafa sabata zitatu zapitazo chifukwa cha mavuto ena. Izi zidachitika sitimayo itangoyenda maola ochepa, patatha miyezi 10 akuikonza. Kukonzako kudadya US$2 miliyoni (zoposa K800 miliyoni).

Mneneri wa kampani yoyendetsa sitimayi ya Malawi Shipping Company adati ayambanso kuikonza zitsulo zina zikafika m’dziko muno.

“Tikuyembekeza zitsulo zimene kampani ya Barloworld ipeze ndipo sitimayi iyambanso kuyenda ikangokonzedwa,” adatero Msowoya.

Iye adati zonse zikayenda, sitimayi ayamba kuikonza Lolemba.

“Aliyense ndi wokhudzidwa ndi momwe zinthu zilili. Ngakhalenso amene amabweretsa zitsulo zikuwakhudza koma tikuchita zotheka kuti sitimayi iyambenso kuyenda,” adatero Msowoya.

Ilala ndi sitima yokhayo yaikulu imene imayenda panyanja ya Malawi.

Sitimayi idayamba kuyenda panyanjayo m’chaka cha 1951 ndipo imanyamula anthu oposa 300.

Related Articles

Back to top button