Chikho cha fodya chasefuka
Chikho cha fodya chaka chino chasefukira ndi makilogalamu 27 miliyoni zomwe zabweretsa nkhawa yoti mtengo wake ukhoza kukhala wonyotsolera ku moto koma alimi anenetsa kuti salola kudyeredwa masuku pa mutu.
Chaka chino, makampani ogula fodya omwe atsika kuchoka pa 10 kufika pa 8 ati ndi wokonzeka kugula makilogalamu 170 miliyoni pomwe alimi akuyembekezeka kukolola fodya woposa makilogalamu 197 miliyoni.

Nduna ya za malimidwe a Roza Fatch Mbirizi adatsegulira msika wa fodya ku Lilongwe Lolemba pa 20 April 2026 koma mkangano pakati pa alimi ndi makampani ogula fodya udayamba tsiku lomwelo.
Chomwe chatosa liombo la alimi kwambiri chaka chino ndi mtengo omwe makampaniwo ayambira kugula fodya wa $2.50 pa kilogalamu poyerekeza ndi $3.20 pa kilogalamu mu 2025 komanso $3 pa kilogalamu mu 2024.
A James Jeke womwe ndi mlimi wa ku Dowa ati nkhawa yaikulu ili poti fodya chaka chino ngwambiri kuposa yemwe makampani adati agula kusonyeza kuti sipakhala kulimbirana fodyayo.
“Mu 2025 komanso 2024, mitengo idaliko bwino chifukwa fodya adali wochepa kuyerekeza ndi fodya yemwe makampani ogula ankafuna ndiye amalimbirana popereka mitengo yabwino koma chaka chino chitionetsa zinthu,” adatero a Jeke.
M’chaka cha 2025, alimi adakolola fodya wokwanira makilogalamu 174 miliyoni pomwe makampani ankafuna makilogalamu 213 miliyoni ndipo mu 2024, alimi adakolola makilogalamu 133 miliyoni pomwe makampani ankafuna makilogalamu 190 miliyoni.
Malingana zochitika za chilengedwe pa msika, malonda akachepa pomwe owafuna ngambiri, mtengo umakwera pomwe malonda akachuluka pomwe owafuna ngochepa, mtengo umatsika.
Koma a Reuben Mnjiraludzu a ku Malingunde ku Lilongwe ati alimi salola kuti zimenezi zichitike chaka chino chifukwa alimi adalowetsa zambiri kuti akolole fodya yemwe akugulitsa ku msikapanoyu.
“Akadayang’ana zomwe tidalowetsa osati zawo zoti fodya wasefukayi chifukwa atipweteka, ambirife tidatenga ngongole za zipangizo komanso tili ndi anthu omwe adatigwirira ntchito ndipo akuyembekeza malipiro awo,” atero a Mnjiraludzu.
A Mbirizi adachenjeza makampani ogula fodya kuti asatengerepo danga kuti kunjaku kuli fodya wambiri kuposa yemwe akufuna kuti apondereze alimi chifukwa kugwa kwa alimi ndi kugwa kwa chuma cha dziko.
“Ngakhale fodya wachuluka, chonde osawapondereza alimi mbali ya mitengo, anthuwa adalowetsa ambiri kuti fodya ameneyu atuluke ndiye akufunika kuti azipezapo kangachepe,” adatero a Mbirizi.
Iwo adaunikiranso bungwe loyang’anira za fodya la Tobacco Commission (TC) kuti lizikambirana ndi makampani kuti atsegule mafakitale opanga ndudu ndi cholinga choti msika wa alimi nawo ukule.
Nkhani ina yomwe yavuta ku msikawu m’sabata yotsegulirayi ndi ya kuchuluka kwa fodya obwezedwa pomwe patsiku lotsegulira msika Lolemba, mabelo 90 mwa mabelo 100 adabwezedwa.
Mkulu wa bungwe la alimi a fodya la Tama Farmers Trust a Abel Kalima Banda adati kuyamba kotero kwa msika n’kobwezera alimi mmbuyo.
“Alimi amadalira msika umenewu pa ntchito yonse yomwe agwira chaka chonse ndiye kumangobweza fodya choncho si bwino, akuluakulu akuyenera alowererepo kuti zimenezi zichepe,” adatero a Banda.



