Nkhani

Kulibe kuzondana kaamba ka kusowa kwa mafuta

Amalawi tsopano ayamba kulingalira mozama asadapange ulendo kuopa kuti angakwangule konse kamthumba komwe khomo likuyang’anira pa zosowa zonse kaamba ka kukwera kwa mtengo wa ulendo.

Izi zadza kaamba kakusowa kwa mafuta a galimoto zomwe zachititsa kuti akathyali pa tauni azibera anthu powagulitsa lita imodzi ya petulo pa mtengo wa K15 000 mmalo mwa mtengo wa boma wa K6 687.

Nawo eni galimoto zonyamula anthu akwenza mtengo wonyamulira anthu a pa ulendo kufika pa mtengo wa chiletso cha ulendowo chifukwa m’madera ena mtengowo wakwera kuposa kawiri mtengo omwe ankayendera m’mwezi wa January 2026.

Mwachitsanzo, ulendo womwe munthu amayendera K5 000 kuchoka ku Area 25 ku Lilongwe kukazonda matenda ku Kamuzu Central Hospital (KCH) nkubwelera, lero akuyenera akhale ndi K10 000 mthumba kuti akazonde matendawo.

Izi zadzetsa nkhawa yoti kuzondana pamavuto ndipamtendere pomwe komwe ndi gawo limodzi lachikhalidwe chathu kukhoza kutha kaamba koti anthu azisinila komwe ali nako n’cholinga choti kawathandize pa zinthu zina zoyenera pakhomo pawo.

“Ngati ndikufuna kukazonda munthu ku Central, ndiyambe ndapanga bajeti ya zotenga yomwe ndi yaikulu kale potengera mitengo ya zinthu kenako ndilingalire zopeza K10 000 yongoyendera. Apapa tikukamba zapafupifupi K50 000,” atero mayi Anet Makawa aku Area 25 ku Lilongwe.

 Maganizo awo agwirizana ndi a Issa Muhammed a ku Area 49 ku Lilongwe komweko yemwe wati masiku ano kuyendera anthu kumudzi kuchoka m’gulu la zinthu zofunika kwambiri pa moyo wa munthu monga ngati zidalili kale.

 “Kale chidali chizolowezi kuti pa chaka makolo amatitengera kumudzi kukaona ndi kudziwana ndi abale athu komanso kukaphunzirako zinthu zina koma pano, ana azibadwa n’kumakalambira m’tauni mommuno ndithu,” atero a Muhammed.

Umboni wina ndiwakuti ulendo wa ndalama zokwana K9 000 (K18 000 kupita n’kubwerera) pa mtunda wa Lilongwe ndi Mchinji m’mwezi wa February 2026, Lolemba lapitali udali K15 000 (K30 000 kupita n’kubwerera).

 Kukwera kwa mtengo woyenderawo kwachitika kutsatira kusowa kwa mafuta agalimoto sabata ziwiri zikuthazi ndipo palibe chilichonse chopereka chilimbikitso kuti vutolo likhoza kutha msanga.

 Nduna ya zofalitsa nkhani a Shadreck Namalomba womwenso ndi mneneri wa boma adati vutoli limeneli ladza kaamba ka nkhondo yomwe dziko la America likuthira dziko la Iran ndi nkhondo zina zomwe zatseketsa njira zodutsamo katundu ochoka kunja ngati mafutawo.

“Vuto limeneli silidagwere ife tokha ayi, lakhudza maiko ambiri. Makampani ambiri ogulitsa mafuta pa dziko lapansi akuopa kudutsa ndi mafuta m’nyanja zikuluzikulu kaamba ka nkhondo ndiye omwe akubwera ochepa kwambiri.

 “Mafutawo akafika ochepa, pakumakhala kukanganirana zomwe zikupangitsa kuti tizigula m’zidutswa komanso pa mtengo wokwera ndiye mutha kuona kuti si vuto lochita kukonza ayi,” adatero a Namalomba.

Iwo adatinso vuto lina ndi loti makampaniwo ayamba kukana kupereka mafuta pa ngongole ndipo mmalo mwake akufuna kulipiriratu pomwe dziko la Malawi lilibe ndalama zakunja zolipilira mafutawo.

Mneneri wa nthambi yoyang’anira za mphamvu za magetsi ndi mafuta la Mera a Fitina Khonje adati bungwelo likuyesetsa kuchita zoti mafuta obwera m’dziko muno azigwirizana ndi mafuta omwe akufunika.

Mizere ya galimoto zopita momwetsera mafuta siyobisanso m’mizinda ndi m’maboma onse m’dziko muno kutsimikizira kuti mafuta kulibeko ndipo Amalawi ofuna maulendo aone chochita.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button