Nkhani

A chakwera sakugawa maswiti

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera achenjeza nduna zawo kuti yense osatha ntchito yake achotsedwa paudindo wake chifukwa nduna zoterozo ndizo zikukolezera moto m’mitima ya Amalawi omwe akukhumudwa ndi kayendetsedwe ka zinthu.

Chomwe chidatsitsa dzaye kuti a Chakwera akwiye chotero ndi mazizi omwe adachitika ku unduna wa zamalimidwe komwe ndalama zankhaninkhani za pulogalamu ya zipangizo zotsika mtengo ya AIP zidasokonekera chifukwa cha ndondomeko zawedewede zogulira katunduyo.

Polankhula ku mtundu wa Amalawi Lachiwiri madzulo, a Chakwera adaimitsa nduna yakale ya zamalimidwe a Lobin Lowe ndi achiwiri awo a Madalitso Kambauwa Wirima ndipo adaponya ku undunawo a Sam Kawale omwe adali nduna ya zamalo.

A Chakwera sadalekere pomwepo koma adauzanso nduna zawo kuti pakubwera m’chokocho wina wa nduna ndipo nduna zonse zomwe zalephera kuwathandiza kukwaniritsa masomphenya awo azithothola n’kuikamo anthu ena omwe angawathandize.

“Amalawi akufuna zotsatira ndipo adasankha kuti ndidzakwaniritse zotsatirazo ndipo ndionetsetsa kuti ndakwaniritsa zotsatirazo ndi inu kapena popanda inu chifukwa sindili pano kunyengerera chipani, nduna kapena mgwirizano. Ndili pano kutumikira Amalawi,” adatero a Chakwera.

Iwo adati akwaniritsa masomphenya wotukula Malawi posalabadira kuti anthu akunena chiyani za iwo kapena akuipitsa bwanji dzina lawo potsogoza ziphuphu kapena kuwawophseza potuma anthu kupanga ziwonetsero zofuna kusokoneza boma.

Izi zakolana ndi zomwe chipani chachikulu chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP) chidapanga popelekera mphamvu ku magulu omwe adakonza zionetsero za Lachinayi zotsutsana ndi momwe zinthu zikuyendera.

M’kalata yake yomwe adasayina ndi a Francis Mphepo, chipani cha DPP chidati chikugwirizana ndi zionetserozo chifukwa boma la Tonse Alliance lanyanya katangale, kusamva komanso kulephera kuyendetsa boma.

“Tikuchenjeza boma la Tonse Alliance kuti lisayerekeze kuponderedza kapena kutsinira zionetserozi kuuna,” idatero kalata ya DPP.

Uthenga wa a Chakwera kwa ndunazo udabwera kutatsala masiku awiri kuti Amalawi achite zionetsero zomwe adakonza ndi magulu ena omwe sakhutira ndi momwe boma la Tonse Alliance likuyendetsera dziko.

Pa za kuchotsedwa kwa a Lowe ndi a Wirima, a Chakwera adati ndunazo zidalephera kukwaniritsa mlingo omwe adazipatsa kuti pofika mwezi wa September, zonse zokonzekera pulogalamu ya AIP zidzakhale zitatha.

“Miyezi 6 yapitayo ndidapatsa unduna wa zamalimidwe malire a September kuti AIP ikhale ili chile koma kufika lero palibe chomwe chachitika. Kwa ine alephera ndipo sindingasekelere kulephera kotere,” adatero a Chakwera.

Iwo adati ndi wokhumudwa kutinso kuundunako kudapezeka nkhani zina zozunguza mutu monga ndondomeko yomwe undunawo udatsata pogula fetereza ku kampani yakunja yomwe idalibe umboni ulionse woti ikhoza kukwaniritsa ntchitoyo nkusokoneza ndalama zokwana K725 miliyoni.

“Tikulondoloza ndalama zimenezi ndipo sitepe yoyamba idali kuthetsa kontirakiti ndi kampani imeneyo, pano mlangizi wa boma pa zamalamulo a Thabo Chakaka Nyirenda ali mkati moyendetsa zoti ndalamazo zibwezedwe ndipo zibwezedwa,” adatero a Chakwera.

Iwo adalimbitsanso mtima Amalawi kuti asade nkhawa za AIP chifukwa komiti yomwe akhazikitsa ikugwira ntchito usiku ndi usana kuwonetsetsa kuti pulogalamuyo isathawane ndi nthawi moti papezeka kale fetereza yemwe Wayamba kale kufika mdziko muno ndipo akhala akufukabe uku akugawidwa mmadera momwe akufunika.

A Chakwera asadalankhule za AIP, Amalawi adali odabwa kuti unduna wa zamalimidwe umabisa nkhani zokhudza pulogalamuyo ngakhale kuululako kuti apindule mupologalamuyo ndi anthu angati.

Koma wapampando wa bungwe la atolankhani a Theresa Ndanga adadzudzula undunawo kuti sumatsatira zomwe lamulo la ufulu otola nkhani (ATI) limanena chifukwa zomwe undunawo unkabisa zidali zofunika Amalawi azidziwa poti pulogalamuyo imayenda ndi ndalama zawo.

Related Articles

Back to top button
Translate »