Achenjeza obwereketsa galimoto: Kuli mbanda
Bambo wina yemwe dzina lake ndi Emmanuel Davie, ali m’manja mwa apolisi pomuganizira kuti adanamiza anthu kuti ndi msilikali wa MDF m’boma la Blantyre.
Bamboyo ndi wa zaka 24 ndipo apolisi ya Limbe mu mzindawo ndiwo adamukwizinga nawo unyolowo.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Limbe, a Mulimbika Chibisa, adatsimikiza za nkhaniyi ndipo adati bamboyo wakhala akubera anthu osiyanasiyana ndipo padakalipano wabera kale anthu ndalama zosachepera K500 000.
Mneneriyo adati a Davie akhala akuvala ngati msilikali ndipo akatero, amapita kwa anthu makamaka okhala ku Bangwe, ndi kumawanamiza kuti iwo ndi msilikali ndipo awapatse ndalama ndi cholinga choti awathandize
A nthu ochita bizinesi yobwereketsa galimoto akuyenera kusamala malingana ndi mchitidwe wa obwereka ena amene akumakapinyolisa kwa akatapira.
Ili ndi chenjezo lomwe apolisi apereka pomwe mchitidwewu ukuchulukira ngakhale kuti iwo alibe manambala a milanduyi.
Apolosiwa aperekanso chenjezoli pomwe sabata ino adagwira bambo wina mu mzinda wa Blantyre pomuganizira kuti adaba galimoto 22 ndi kukapinyolitsa kwa akatapira osiyanasiyana.
Malingana ndi mneneri wa apolisi m’chigawo cha kumwera Mayi Beatrice Mikuwa, apolisi adamanga a Mustafa Charles a zaka 22 omwe akuwaganizira kuti adabwereka galimoto 15 ku kampani imodzi yobwereketsa galimoto ya Success Civil and Auto Mobile pamene ena 7 adabwereka kwa anthu osiyasiyana.
“Woganiziridwawa amakasinthitsa umwini wa galimoto ndipo amakapereka ngati chikole kwa anthu akatapira. Malingana ndi zomwe tapeza, iwo pamodzi adakatenga ngongole zoposa K14 miliyoni,” adatero a Mikuwa.
Malingana ndi a Mikuwa, apolisi adayamba kufufuza za nkhaniyi atalandira madando kuchokera kwa anthu omwe woganiziridwawo adakatenga.
Pomwe iwo adayamba kufufuza ndi pamene adapeza kuti A Charles adatenga galimoto zochulukwa kwa anthu ena omwe amafufuza. Pofika Lachinayi sabata yatha, woganiziridwawa adali asadapite ku bwalo la milandu kukaonekera chifukwa apolisi adali akufufuzabe nkhaniyi.
Koma akuluakulu a kampani ya Success Civil and Auto Mobile sadapezeke kuti athirepo ndemamga pa nkhaniyi.
Aka sikoyamba kuti apolisi amange anthu powaganizira kuti akuchita zoterezi. Miyezi iwiri yapitayo, apolisi mu mzinda wa Lilongwe adamanaga anthu ena awiri powaganizira kuti amakapinyolitsa galimoto kwa akatapira posinthitsa umwini wa galimotozo.
Mmodzi mwa obwerekesa galimoto mu mzinda wa Blantyre omwe adaberedwapo, a Charles Zalira, ati iwo sadaganizepo kuti aberedwa pomwe ankabwereketsa.
A Zalira, omwe amakhala ku Nancholi mu mzindawu, adati chomwe chidawadabwitsa n’choti galimoto ya mtundu wa Suzuki Splash yomwe adabwereketsa idasinthidwa umwini ngakhale iwo sadakasindikize chala ku Road Traffic.
“Munthu yemwe adandibera galimotoyo pobwereka adanama kuti layisensi yake wasiya ku nyumba koma iwo adaperekeratu ndalama za masiku 5.
“Monga njira imodzi yomwe ndimatsata pobwereketsa galimoto, munthu amayenera apereke layisensi yake kuti ndijambule monga chitsimikizo kuti munthuyu si wakuba komanso kuti zingakhale zophweka kumupeza atakhala kuti wasowa,” adatero a Zalira.
Iwo adati adalimba mtima kupeza mwayi wa ntchito ya usilikali ku MDF.
Koma litakwana tsiku la 40, lomwe lidali pa 18 May 2025, bamboyo adanjatidwa anthu atawatsina khutu apolisiwo za nkhaniyo.
“Zitafika poti anthu ayamba kudabwa nawo mchitidwe wa bambo Davie maka posonyeza ngatidi ndi msilikali wochokera ku MDF, sadachedwe koma kukamuneneza ku polisi ya Bangwe komwe apolisiwo adayesa kufufuza za mkuluyo. Ndipo kumapeto kwa kafukufukuyo, iwo adapeza kuti bamboyo samagwira ntchito ku nthambi ina iliyonse ya MDF m’dziko muno. Motero, padakalipano akusungidwa m’chitokosi,” adatero a Chibisa.
Iwo adatsindika kuti bamboyo akaonekera ku bwalo la milandu akamaliza kafukufuku wawo kuti akayankhe mlandu wobera anthu powanamiza kuti ndi msilikali.
A Emmanuel Davie amachokera m’mudzi mwa Malata, m’dera la T/A Makuwira, m’boma la Chikwawa.