Banja ndalilephera
Anatche, muli bwanji? Ine mavuto.Banja ndidalikondetsetsa koma ndikuona ngati ndililephera.
Ndili pa banja ndipo tili ndi ana awiri. Wina wamaliza ku sukulu ya ukachenjede. Wina wangoyamba kumene.
Ine mmene ankandikwatira amuna anga ndidali Ndikugwira ntchito yabwino kwambiri. Kotero kuti zinthu zambiri pakhomopo ndimapanga ndine chifukwa choti anzanga samalandira ndalama zambiri. Kwa ine, silinali vuto chifukwa amuna anga ndimawamvetsetsa.
Ine ndidagula nyumba komanso galimoto. Amuna anga ndiwo amayendera galimoto chifukwa ndidali ndikuyendera ya ku ntchito kwanga komwe ndidali manejala.
Maphunziro a ana athu amalipira ndi a ku ntchito kwathu komanso zinthu ngati madzi, magetsi ndi zina zambiri.
M’chaka cha 2021, ntchito yanga idatha chifukwa cha matenda a Covid 19 pomwe kampani yathu adaitseka.
Nthawi imeneyo n’kuti amuna anga atakwera kwambiri udindo ku ntchito kwawo.
Amuna anga adayamba kunyada ndi kusagwirika. Adayamba kundinyoza ndi kusandikonda.
Ndalama za ndiwo ndi zogulira zinthu zina ndimachita kumapempha ngati kuti sakudziwa kuti anthu amayenera kudya.
Suluku fizi ya ana ndimachita kupempha mowapembedzera ngati kuti ana siawo. Akamapereka uku akuyankhulira!
Izi zakhala zikuchitika nthawi yaitali.
Ndidakhala ndikuwadzudzula komanso kukambirana nawo za makhalidwe awowa koma samasintha.
Ndidapita kokasuma kwa ankhoswe komanso ndidakhala ndikuwauza akwawo za khalidwe lawoli koma samasintha. Amangoyankha zodziwa okha.
Nthawi yonseyi ndidali ndikufufuza ntchito koma siyimapezeka.
Chaka chatha ndidapeza ntchito ina ndipo ndi yabwinonso. Pakuti ndidali nditatopa ndi zochita zawo, ine ndidasamuka m’nyumba mwawo ndi kukapeza nyumba yanga.
Nditangochoka, iwo ntchito inatha. Ndiye pano akufuna kuti azidzakhala m’nyumba mwanga.
Anatche, ine bambo amenewa sindikuwafunanso. Banja limeneli latha. Ndikupita ku khoti kokathetsa ukwatiwu.
Kodi pamenepa ndikulakwitsa? Komanso kodi aiwala zomwe amandipanga ine ndisali pa ntchito? Ndakoma lero chifukwa ndapeza ntchito ina?
Ndilangizeni ngati ndikulakwa.
Amuna anu Mwina mawaya ena sakugwira. Mwawachitira zambiri zabwino komanso kuwaphimba kuti asaonekere ng’amba. Zonsezo adayenera kuyamika komakuonetserani chikondi. Inu ndi mkazi wabwino kwambiri. Si akazi ambiri omwe angamugulire galimoto mwamuna wawo.
Chifukwa chosowa chikondi n’chifukwa chake ntchito yawathera.
Amenewotu muwasiye kuti avutike kaye pang’ono kuti azindikire ndi kukumbukira zoipa zomwe amakuchitirani. Kenako mudzawakhululukire.
Popeza amati choipa sitibwezerana.
Anatchereza.