Adandaula za misewu yosakonzedwa
Pomwe anthu akhala akuitsotsombetsa nthambi ya Road Fund Administration ati ponena kuti ikukanika kukonza misewu ya m’dziko muno chonsecho nthambiyo imatolera ndalama zankhaninkhani kudzera m’zipata za Chingeni ndi Kalinyeke Toll Gates, boma lakhala likukhalira ndalama za msonkho wa ku mafuta a galimoto pogula wa fuel levy kwa zaka pafupifupi zitatu zapitazo tsopano.
Kufikira lero, bomalo lili ndi ngongole pafupifupi K218 biliyoni ya mtunduwu yoti lipereke ku nthambi ya RFA, zomwe ena anena kale kuti zikadatha kusintha nkhope ya misewu yambiri m’dziko muno.

shows city roads faced
biggest underfunding
Izi zadziwika pomwe bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (Cdedi) lidakayendera malo awiriwa potsatira ganizo loti nthambi ya RFA yakonza zokweza mitengo ya ndalama zomwe amagalimoto amapereka podutsa pa zipatazo, kuyambira pa 1January chaka chikudzachi.
Malinga ndi mkulu wa RFA a Stewart Malata, ndalama zomwe zimatoleredwa pa zipata za Chingeni komanso Kalinyeke n’zosanunkha kanthu pa mavuto a misewu ya m’dziko muno, yomwe mkuluyo adavomereza kuti yambiri idaduga.
“Tidziwenso kuti pa lamulo, ndalama zotoleredwa pa toll gate zimayenera kupindulira msewu omwe toll gate-yo ili, osatinso kupangira chitukuko cha misewu ina. Choncho, msewu wa M1 ndiye woyenera kudyerera pa chitukuko chochokera ku ma toll gate athu awiriwa.
“Mukaonetsetsa, ndalama zachepa, mavuto a msewu wathu ndi ambiri. Ichi n’chifukwa tikulingalira zokweza mitengo kuti mwina kotoleredwako kagwirizaneko ndi momwe mitengo ya katundu ndi zipangizo za chitukuko cha msewu ilili padakalipano. Komanso, zikadatichitira ubwino tidakaonjezeranso ma toll gate m’misewu ina monga ya Mzuzu-Salima, Lilongwe-Mchinji komanso Kasungu- Mzuzu kuti kathumbako kapindulirenso misewu inayo,” adatero a Malata.
Iwo adati ntchito yomanga ma toll gate atsopanowo bwenzi pano ili pena, angaponso mwina atatha nkuyambanso kugwira ntchito, koma kuti boma pena silimachita mbali yake yoyenera mzaka zapitazo.
Mwachitsanzo, iwo adati boma lakhala lisakupereka ku nthambi yawo ndalama ya msonkho pa mafuta a galimoto ya fuel levy m’zaka zoposa ziwiri zomwe ndalamayi yakhala isakutuluka.
“Mutati muone, imeneyi ndi ndalama ndithu yoti ikadatha kuchita zitukuko zingapo za misewu yathu. Apa tisaname, tidabwerera mmbuyo ndipo pomwe timatero, ukunso misewu yathu imanka igugiragugira,” adafotokoza motero.
Mkulu wa bungwe la CDEDI a Sylvester Namiwa ati n’zodandaulitsa kuti boma lidatsogoza ndale kulekana ndi umoyo wa anthu ake, ponena kuti chitukuko cha misewu imene idakakonzedwa ndi ndalama za msonkho wa ku mafuta a galomotowo ndiye ngodya ya maufulu ambiri a anthu, kuphatikizapo ufulu wolandira thandizo la za umoyo mu nthawi yake.
“Komanso nanu mwakhala mukumagwira ntchito panokha, chonsecho ndinu otumidwa ndi Amalawi iwo eni. Izizi bwenzi zitapeweka mwachangu mukadakhala kuti munkachita zinthu zanu pachione. Kusintha kukadakhalapo ndithu. Ngati ndi phokoso, anthu tikadapanga ndithu kuti zinthuzi zizioneka phindu lake kwa mtundu wa Amalawi,” a Namiwa adatero.
Mkulu wa bungwe la Road Authority, a Amiel Champiti, ati iwo adapeza kale kampani zomanga ma toll gate atsopanowo, ndipo ina mwa ntchitoyo bwezi itatsirizika pofika pano boma lidakakhala kuti lapereka ndalama za misonkho ya ku mafuta a mzakazi, monga momwe zimayenera kukhalira.
Bungwe la Cdedi lidalangiza kuti kunka mtsogolo, RFA ikuyenera kuika zinthu zake poyera, makamaka ndalama zomwe zizitoleredwa pa m’ma toll gate komanso kuti zagwira ntchito yanji, kuti Amalawi azidziwa ndi kuyamikira ntchito ya thukuta lawo poyenera kutero.



