Mafumu, a m’boma apezeka mu Fisp
Nduna ya za malimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi Mayi Roza Mbirizi ati athana ndi ogwira ntchito m’boma omwe ayerekeze kugula zipangizo za u limi zotsika mtengo m’pulogalamu ya Fisp.
A Mbirizi adanena izi ku Lilongwe pomwe amapereka tsatanetsatane wa momwe pulogalamu ya Fisp ikuyendera ndipo adati n’zokhumudwitsa kuti mafumu ena akudziika okha pa mndandanda wa olandira.

“Ogwira ntchito m’boma 3 800 adadziika okha pa mndandanda ndipo ngati asadagule zipangizozo asayerekeze kutero chifukwa tiwatsatira kulikonse komwe aliko ndipo lamulo lidzagwira ntchito,” adatero a Mbirizi.
Chaka chino anthu 1.1 miliyoni ndiwo akuyembekezeka kupindula mu Fisp zomwe nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha adati zidachititsa kuti boma lionjezere bajeti m’pulogalamuyo.
A Mbirizi adapitirira kuulula kuti mafumu ena ndi ogulitsa zipangizozo akupanga chinyengo pomaumiriza alimi kuti aziwaonjezera ndalama chonsecho mtengo wa thumba limodzi la fetereza udaikidwa pa K10 000.
Nduna ya maboma aang’ono a Ben Phiri nawo aopseza kuti akhaulitsa fumu yomwe ipezeke ndi mlandu wokhudza pulogalamu ya Fisp yomwe cholinga chake n’kuthandiza alimi ovutikitsitsa.
“Mfumu imayenera izikhala yachitsanzo chabwino osati yoyambitsa zoipa ndiye mukangopezeka kuti mukukhudzidwa n’kusokoneza Fisp, dziwiranitu kuti tikulandani maudindo tipatse ena akhalidwe la bwino,” adatero a Phiri.
Chaka chilichonse, pulogalamu ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo imakumana ndi zipsinjo zomwe zimachititsa kuti alimi ena oyenera kupindula asapindule, komanso anthu a ndalama zawo amanyengerera alimi n’kumawagula makuponi.
Koma mmodzi mwa akuluakulu amabungwe a Michael Kaiyatsa ati nkhani zomwe zamvekazo n’zofunika kufufuza n’kulanga anthu osayenera kupezeka pa mndandanda koma apezekapo chifukwa ndi umboni woti padachitika za chinyengo.
A Mbirizi adati mwa anthu 1.1 miliyoni omwe akuyembekezeka kupindula, anthu 131 184 adagula kale zipangizo zawo ndipo fetereza wamatani 37 818 ali kale mosungira pomwe matani 10 949 ali m’njira kuchokera ku Zambia ndipo matani 62 000 boma ligula kwa amabizinesi mdziko mommuno omwe ali ndi fetereza.
Nthawi zambiri, fetereza wa Fisp amafika mochedwa m’madera ena makamaka akumidzi kwambiri ndipo akadaulo akhala akuunikira kuti boma lizikonzeratu mapulani oti zipangizozo ziziyamba kupezeka mvula isadagwe.
Koma pomwe malipoti akusonyeza kuti mwa anthu 1.1 miliyoni, anthu 131 184 ndiwo agula kale, mvula yagwa kale ndipo m’madera ena mbewu monga chimanga zidamera moti pompano alimi ayamba kufuna kuthira fetereza.



