Nkhani

Bilu ya CDF yadutsa popanda wotsutsa

Aphungu a Nyumba ya Malamulo dzana adutsitsa bilu yomwe akufuna kuti apitirize kuyang’anira zitukuko za ndalama za Constituency Development Fund (CDF) yomwe khothi lidalamula kuti isamawakhudze.

Khoti mwezi wa May lidagamula kuti aphungu a Nyumba ya Malamulo asamayendetsenso CDF komanso asamatenge nawo gawo pa zokambirana za chitukuko chokhudza CDF pa khonsolo.

Imodzi mwa ntchito za CDF

Koma dzulo pogwiritsa ntchito mpata omwe aphungu amabweretsa mabilu omwe akufuna, phungu wa kummwera kwa boma la Mzimba a Emmanuel Chambulanyina Jere adabweretsa biluyo yomwe poyamba idaponyedwa ku komiti ya za malamulo kuti ikaunikidwe.

Aphungu onse omwe adalipo 199 adagwirizana ndi biluyo kuti idutse zomwe a Jere adasangalala nazo ponena kuti zikutanthauza kuti aphungu ali ndi chidwi chotukula madera awo kudzera mu CDF.

“Momwe zayendera, zaonetsa kuti aphungu aikonda bilu imeneyi, mwaona momwe avotera kuti idutse. Apapa zikutanthauza kuti bilu yadutsa ndi mphamvu zambiri,” adatero a Jere.

Koma akuluakulu ena omwe akhala akudzudzula biluyo atemetsa nkhwangwa pa mwala kuti atengera biluyo ku khoti kuti akaitsutse kaamba koti akuona kuti aphunguwo ali ndi zolinga zina pa ndalamazo.

Mkulu wa bungwe loona za makhonsolo la Malga a Hardrod Zeru Mkandawire komanso mkulu wa mabungwe oima paokha omwe amayang’anira za zochitika m’dziko la National Advocacy Platform (NAP) a Benedicto Kondowe anenetsa kuti nkhaniyi siithera pompa.

“Chomwe sitikumvetsa ndi khama lomwe ali nalo kuti aziyendetsa CDF, pali chiyani chomwe awonamo? Khoti lidawaletsa, mabungwe akhala akuwalangiza koma achitabe zofuna zawo ndiye ife tingopita nayo ku khothi basi,” adatero a Mkandawire.

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika posachedwapa adalengeza kuti ndalama ya CDF ikwera kuyambira bajeti ya chaka cha mawa kufika pa K5 biliyoni kuchoka pa K2 miliyoni ndipo malingana ndi chigamulo cha khoti komanso zofuna za mabungwe, ndalamayo aziyendetsa ndi akuluakulu a pa khonsolo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button