Akachasu nawo akulira ndi kukwera kwa shuga
Mwina n’kumaona ngati amene amakonda za tseketseke monga tiyi ndi makeke okha ndi amene akulira ndi kusowa komanso kukwera mtengo wa shuga. Nawo okonda za tsooo monga kachasu akulira chifukwa mtengo wa bibida nawo wakwera.
Mayi Fatness Timoteyo, omwe amatchuka kuti Mayi Chipoya m’mudzi mwa Mwafumbi kwa T/A Makhuwira ku Chikwawa ati kukwera mtengowu kwachititsa kuti achepetse kachasu yemwe amatcheza komanso kukweza mtengo wa chakumwa choongola nkhopechi.

“Pakatipo ndinasiya kaye kuphika kachasu kwa sabata ziwiri malinga ndi kukwera mtengoku. Nanga mpaka K7 000 paketi imodzi! Paketi imodzi ya shuga imatulutsa maveta awiri,” adatero mayiwa.
Komatu makasitomala ake amamuvutitsa koma adawauziratu kuti akweza veta ya kachasuyo kuchoka pa K4 000 kufika pa K4 300.
“Izi tachita potengera kuti kupatula kukwera mtengo wa shuga, nacho chimanga chidakali chokwera mtengo kuno kwathu,” adatero iwo.
A Chipoya omwe adayamba bizinezi yotcheza kachasu m’chaka cha 1986 akudabwa ndi kukwera mtengo kwa shuga komwe kwachitika chaka chino ndipo apempha adindo kuti achite machawi pokonza mtengo ofikirika wa shuga.
“Shuga amagwira ntchito zosiyanasiya kupatula kuthandiza ife a mabizinesi chonchi pomwe mtengo wakwera zikutanthauza kuti anthu ambiri asiya kumwa tiyi, ana sazidya phala ndiye kutinso matupi awo sazikhala athanzi. Pakufunika kuchita machawi pothana ndi vutoli,” adatero iwo.
Ndipo Chisomo Masamba, yemwe amakhala ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre wati kukwera mtengo wa shuga kwachititsa kuti ophika akweze zomwe zamukhudza ngati wooda.
“Mwezi wa April, mutu wa kachasu timaoda K6 000 pa lita iliyonse ndipo timapindula. Koma pano botolo lomwelo tikuoda K9 000. Ndiye nafenso takweza,” watero Masamba.
Vuto la kusowa kwa shuga lakhala likuzunguza Amalawi kwa sabata zingapo tsopano ndipo zithunzi za mizere ya anthu odikilira kugula shuga zakhala zili yambakata m’masamba a mchezo.
Mmbuyomu, kampani yopanga shuga ya Illovo idalengeza kuti kusowa kwa shuga kwadza kaamba ka anthu ena amene akumamugulitsa kunja kwa dziko lino.



