Nkhani

Akana ndalama za Covid-19

Listen to this article

Anthu ayera m’manja. Ndalama za Covid zatuluka. Komatu mayi wina mumzinda wa Mzuzu wakana kulandira ndalamazi akuti nzasataniki.

Mayiyo akuti ndalamayi ikatuluka aipereka kwa mnzake.

Malinga ndiGertrude Moses, mnzakeyo adamuuza kuti sangatenge ndalama zomwe a boma akupereka kuthandiza anthu pa chuma m’nyengo ino ya matenda a Covid 19 pa zifukwa zitatu.

“Anati ndalamazi ndi za sataniki komanso za kumidima chifukwa zangobwera osakhetsera thukuta,” adalongosola Moses.

Iye adatinso akuopa kulandira ndalamazi chifukwa mwina ndi nyambo ndipo mtsogolo muno aboma adzalengeza kuti  aliyense yemwe adalandira azikasamalira odwala matendawa.

Komatu si mayi yekhayu yemwe ali ndi maganizo achoncho chifukwa nawo omwe ankachita kalemberayu mumzinda wa Mzuzu adakumana nazo zambiri.

Malinga ndi mmodzi mwa omwe ankachita nawo kalemberayu, Mirriam Masangano makomo ambiri amabwenzedwa kuti ndondomekoyi ndi ya sataniki.

“Anthu ena ambiri adakananso kulembetsa maina awo chifukwa amati ali kale ndi ndalama ndipo ena olo mpanda sankatitsekulira,” adalongosola Masangano.

Iye adati mnzawo wina mpaka adalumitsidwa galu pogwira ntchitoyi.

Pomwe mnzake wina  Kiloshina Kampani adati m’makomo ena amalandiridwa ndi agalu omwe amawathamangitsa mpaka kugwa  ndi kuvulala.

“Tikukhulupilira kuti izi zidachitika chifukwa anthuwa adalibe uthenga wokwanira wokhudza ntchitoyi,” adalongosola Kampani.

Mneneri wa khonsolo ya mzinda wa Mzuzu, MacDonald Gondwe adati ngakhale khonsoloyo idayesetsa kulengeza pa mkuzamawu za kalemberayu, ambiri sadamvetsetse.

“Ndi zoona kuti ntchitoyi idakumana ndi zokhoma zambiri ndipo madandaulo ngosayamba kuchokera kwa omwe amagwira ntchitoyi komanso olandira,” adalongosola Gondwe.

Iye adati ena mwa omwe adakana kulandira ndalamazo, pakadalipano akuvutanso kuti alowe nawo mkaundula wa opindura nawo pa ndalamazi.

Pomwe Gilbert Kaponda yemwe amagwira ntchito ndi anthuwa mzinda wa Mzuzu  kuchokera ku unduna woona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo adatsimikiza kuti anthu awo adakumana ndi mavutowa.

Mmodzi mwa ogwira ntchito athu ankafuna kumenyedwa, bambo wa panyumbapo atamupezelera akumufunsa mafunso mkazi wake. Bamboyu amayesa kuti mkazi wake amafunsiridwa,” adalongosola Kaponda.

Anthu papafupifupi 199 000 m’dziko muno apindula nawo pa ndondomeko ya boma yomwe ikupereka ndalama zokwana K19.5 billion zothandizira anthu omwe kapezedwe kawo ka chuma kakhudzidwa kwambiri ndi matenda a Covid 19.

Ndalamazi ziperekedwa kwa miyezi itatu kwa anthu okhala madera a Zomba, Mzuzu , Blantyre ndi Lilongwe. Ndipo azilandira K35 000 pa mwezi.

Pomwe anthu a ku Lilongwe ndi Blantyre ayamba kale kulandira zawo, ku Mzuzu ndi Zomba sizidayambe.

Related Articles

Back to top button
Translate »