Nkhani

Akhumudwa ndi kusowa kwa mnyamata wachialubino

Magulu omenyera ufulu wa anthu komanso bungwe la anthu achialubino la Association for People with Albinism in Malawi (Apam) ati ndi okhumudwa ndi kusowa kwa mnyamata wa chialubino mwezi wa January m’boma la Mangochi.

Mneneri wapolisi m’chigawo cha kummawa Inspector Joseph Sauka watsimikiza kuti Daiton Saidi wa zaka 18 adasowa pa 27 January 2021 ndipo apolisi adamanga anthu atatu omwe akuwaganizira kuti ndiwo adasowetsa mnyamatayo.

Simbota: Chitetezo Chikhalepo

“Tawafunsa ndipo akuvomera koma sitilankhula zambiri chifukwa tikadafufuza ndiye tingasokoneze kafukufuku,” adatero Sauka.

Izi zikuchitika patangotha miyezi 7 chilowereni boma la Tonse Alliance lomwe munsanamira za kampeni yake inkatsindika mfundo yokhwimitsa chitetezo cha anthu achialubino.

Lonjezoli lidalandiridwa ndi manja awiri chifukwa lidabwera pomwe pafupifupi sabata ziwiri zilizonse kumasowa kapena kuphedwa munthu wachialubino ndipo mabungwe komanso maiko ankadzudzula dziko la Malawi chifukwa cholephera kuteteza anthuwo.

Koma Pulezidenti wa Apam Ian Simbota wati bungwelo ndi lodabwa kuti chisadathe ndi chaka chomwe, mchitidwewo wayambiranso.

“Mitima yathu idayamba kukhazikika chifukwa timakhulupilira kuti boma likwaniritsa lonjezo lake la pakampeni koma momwe zachitikiramu mantha athu abwereranso ndipo tikufuna chitetezo chathu chikhwime monga momwe adatilonjezera,” watero Simbota.

Mabungwe a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) ndi Centre for the Development of People (Cedep) ati potsatira nkhondo yomwe yamenyedwa mmbuyomu, zosowetsa ndi kupha anthu achialubino zimayenera kutha.

“Nzomvetsa chisoni kuti kufika lero, msika wa ziwalo za anthu achialubino ukadalipo. Apolisi akuyenera kuchitapo kanthu kuti mchitidwewu uthe msanga,” yatero kalata yomwe mabungwewo atulutsa.

Mabungwewo ati boma likuyenera kuyamba kugwiritsa ntchito ndondomeko yotetezera anthu achialubino yomwe idakonzedwa mchaka cha 2015.

Mchitidwe osowetsa ndi kupha anthu achialubino udafika pachimake kuyambira m’chaka cha 2014 ndipo boma lidalamula kuti milandu yokhudza nkhanzazi iziweruzidwa ndi khothi lalikulu lomwe lili ndi mphamvu zopereka chilango chachikulu.

Kufikira lero, milandu yokhudza kusowetsa ndi kupha anthu achialubino yomwe idalembetsedwa mukhothi ilipo 169 ndipo milandu 43 mwa iyo idagamulidwa kale.

Mirandu 17 idatsekedwa pomwe milandu 40 ikadali mukhothi, ina iwiri yapsa kale kuti ikhoza kupita kukhothi pomwe milandu 62 ikadafufuzidwabe.

Chodabwitsa nchakuti chiyambireni kafukufuku wa polisi komanso komiti yomwe Pelezidenti wakale Peter Mutharika adakhazikitsa ndipo imatsogoleredwa ndi Dr Hetherwick Ntaba, msika waziwalo za anthu achialubino sudziwikabe komwe ulili.

Malingana ndi Sauka, Saidi adasowa pa 27 January 2021 ndipo amachokera mmudzi mwa Kate Kadewere kwa T/A Chowe m’boma la Mangochi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button