Nkhani

Kulankhula ndi Habakuku, K1 miliyoni igwe kaye

Masiku apitawa, mtsogoleri wa mpingo wa ECG-Jesus Nation a Shepherd Bushiri adapereka K6 miliyoni kwa Prophet Habakuku, yemwe amatchuka pa masamba a mchezo atamupempha K500 000.

Koma pasanathe sabata imodzi, masamba a mchezo adagundika ndi kanema amene Habakuku adadzijambula akunena kuti ndalamayo yatsala K1.5 miliyoni yokha.

Habakuku: Sindilankhula ndi atolankhani ulele

Pofuna kumva zambiri, za momwe zidakhalira, Habakuku, yemwe dzina lake lenileni ndi Stanford Sinyangwe, adati: “Sindilankhula ndi atolankhani ulele. Tumizani K1 miliyoni. Kapena tumizani K500 000 ku Airtel Money.”

Koma tisanapitirize kufunsa zambiri, anadula foniyo.

M’kanema imene adatulutsa sabata yatha, Habakuku adati pa ndalama imene adapatsidwayo, adagula malo a K3.5 miliyoni ndipo K1 miliyoni adaigawa kwa abale ndipo K1 miliyoni adayisunga kubanki. Kanemayo adadzetsa mpungwepungwe m’masamba a mchezo, makamaka pomwe iwo akufotokoza za maloto awo pomwe akupempha thandizo lina.

“Ndikufuna kumanga nyumba yaikulu, ya zipinda 8 imene chipinda chilichonse chizikhala ndi bafa komanso chimbudzi. Komanso pamalopo padzakhalanso ma boys quarter 10 azipinda zitatu iliyonse,” adatero iwo.

Mu uthengawo, iwo adapitirira kufotokoza kuti pakadalipano ali ndi lingaliro lofuna kuyamba kuumba zidina ndipo ali ndichikhulupiliro choti a Bushiri awathandiza ponena kuti akudziwa kuti Mulungu wa a Bushiri salephera.

Iwo adamema Amalawi kuphatikizapo mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti atengere chitsanzo chomwe a Bushiri aonetsa powathandiza.

“Tikupempha bambo athu a Chakwera komanso mayi athu a Monica Chakwera kuti atitumizire chuma choti tigwiritse ntchito pomanga nyumba. A Malawi, a Mikozi, a Mibawa, a MBC komanso a Zodiak chitanipo kanthu,” adatero iwo.

M’kanema wina amene tidamuona, kumapemphero amene adali ku Mzuzu, a Bushiri adaitanitsa a Habukuku kuti abwere kutsogolo komwe adawauza kuti awapatsa K6 miliyoni.

“N’zapamwamba kukumana ndi munthu uyu wa Mulungu. Ndimamukonda, nayenso amandikonda,” adatero a Bushiri, uku opemphera mumpingomo akuimba nyimbo ya Lero lero lero!

Yemwe amalankhulira mneneri Bushiri a Aubrey Kusakala adapempha abale awo a mneneri Habakuku kuti azitha kuwaunikira kagwiritsidwe ntchto kabwino ka ndalama.

“Sitingawapangire chiganizo pa kagwiritsidwe ntchito ka ndalama koma chikutisangalatsa ndi choti mneneri Bushiri adachita chithu chabwino powathandiza monga mneneri wa Mulungu.

“Tikukhulupirira kuti pempho lomwe labwera kudzera pa kanema wasopanoyi likupita kwa Amalawi onse ndipo tikulimbikitsa Amalawi kuti tiyeni timuthandize munthuyu,” adatero a Kusakala.

Iwo adatinso a Bushiri adathandiza mneneriyu ndi ndalama yokwana K6 miliyoni komanso kuti adawagulira zida zogwirisa ntchito potumikira Mulungu monga chinkuza mawu zomwe ndi zokwana K400 000 komanso kuti adawaunikira momwe angasamalire ndalama zawo.

Malinga ndi zimene adalankhula pa kanema ya Zodiak ndi Joab Chakhaza, a Sinyangwe adati siali pabanja ndipo amachokera m’dera lotchedwa Mselema ku Chitipa. Ali ndi ana awiri.

Sukulu adalekera Fomu 2 ndipo adaphunzira zaubusa ku Pentecostal Holiness Association ndipo adayamba ubusa ku Pentecost Assemblies of Malawi asanayambitse utumiki wawo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button