Adzudzula mawu a APM
Akadaulo pa ndale komanso mabungwe omwe si a boma omwe amaunikira za kayendetsedwe ka zisankho ati mawu onyozana kapena kufalitsa mphekesera zopanda umboni zingasokoneze ndale komanso kayendetsedwe ka zisankho.
Iwo amalankhula ndi Tamvani zokhudza uthenga omwe mtsogoleri wachipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) a Peter Mutharika adauza anthu pa msonkhano omwe adachititsa Lamulungu pa Njamba ku Blantyre.
Mwa zina, a Mutharika adati akudziwa zoti chipani cha Malawi Congress (MCP) chikukonza zodzabera chisankho cha 2025 pogwiritsa ntchito nzika za ku Mozambique komanso mpingo wina omwe sanautchule.
Iwo adapitiriza kuuza anthu omwe adabwera pamsonkhanowo komanso omwe adatsatira msonkhanowo kudzera munjira zosiyanasiyana zofalitsira uthenga kuti chipani cha MCP chidaika malire kuti zipani zina sizingakapange msonkhano kapena kampeni pachigawo chapakati.
Mneneri wa mgwirizano wa mabungwe omwe si a boma koma amaunikira pa za kayendetsedwe ka zisankho a McBain Mkandawire ati andale ali n’chizolowezi chonena zilizonse akakomedwa pamsonkhano.
“N’zomvetsa chisoni kuti zikuchokera kwa atsogoleri yemwe timayembekeza kuti akudziwa tanthauzo la ndale kuti n’kupikisana pa mfundo ndiye mmalo monena mfundo zoona atsogoleri azitaya nthawi n’kufalitsa mphekesera?” adatero a Mkandawire.
Iwo adatinso mabungwe omwe si a boma ndi okhumudwa kuti
zoterezi zikuyambika ngakhale nyengo ya kampeni siyinafike zomwe zingachititse kuti anthu alowe nyengo ya kampeni ndi mangawa.
Pa mphekesera zofuna kubera chisankho cha 2025, a Mkandawire ati ngati a Mutharika ali ndi umboni wa mphekeserazo, njira yabwino akuyenera kukadandaula ku bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).
” Tonse tikudziwa kuti milandu kapena madandaulo okhudzana ndi chisankho amapita ku bungwe la MEC ndipo ngati pali umboni, bungwelo limadziwa kaweruzidwe pogwiritsa ntchito malamulo azisankho,” adatero a Mkandawire.
Kadaulo pa ndale George Chaima adati a Mutharika samayenera kulankhula zoti anzawo akuwadulira malire chifukwa m’dziko muno mulibe chipani chomwe chili ndi mphamvu zodula malire ochitira ndale.
“Zimenez i zikhoza kungodzetsa chisokonezo pakati pa otsatira zipani zosiyanasiyana chifukwa ena atakhulupilira kuti chipani chawo chikuduliridwa malire, sangakondwe. Komanso Malawi ndi mmodzi,” adatero a Chaima.
Nawo a Ernest Thindwa adati uthenga odzetsa mkwiyo ulionse pamsonkhano wa ndale ndi wosaloledwa chifukwa ukhoza kusokoneza ndondomeko yonse ya chisankho.
Mneneri wa boma a Moses Kunkuyu omwenso ndi nduna ya zofalitsa nkhani adati boma limayembekezera atsogoleri monga a Mutharika kukhala patsogolo kulimbana ndi ndale za ziwawa.
“N’zomvetsa chisoni kuti mawu ngati amenewo n’kuchokera kwa mtsogoleri chifukwa timayembekeza kuti atsogoleri ndiwo azikhala oyanjanitsa osati odanitsa kapena wodzetsa chisokonezo,” adatero a Kunkuyu.
Pamsonkhanowo, a Mutharika adauza anthu kuti pavute olo pasavute iwo adzapambana chisankho cha 2025 ndikubweleranso m’boma momwe adalamulira kuyambira chaka cha 2014 mpaka 2019 ndipo adagwa pachisankho cha chibwereza mu 2020.