Nkhani

Amalawi alemekeza Bingu

Listen to this article

Amalawi m’zigawo zonse m’dziko muno apereka ulemu wawo wotsiriza kwa yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino, Bingu wa Mutharika.

Mutharika adamwalira pa 5 Epulo atadwala mtima.

Thupi lake lomwe lidatengeredwa m’dziko la South Africa, lidafika m’dziko muno Loweruka pa 14 kudzera pabwalo la ndege la Kamuzu mumzinda wa Lilongwe.

Kuyambira Loweruka mpaka Lasabata, akuluakulu aboma ndi abanja motsogozedwa ndi mtsogoleri wadziko lino, Joyce Banda, adapereka ulemu wotsiriza kwa malemuwa.

Lolemba pa 16, thupili lidatengedwa ku Nyumba ya Malamulo mumzindawo komwe Amalawi akuchigawo chapakati adapereka ulemu wawo mpaka pa 17.

Thoko Loga wa ku Kawale yemwe amapenta galimoto adati adzakumbukira Mutharika kumbali ya chimanga komanso kumangidwa kwa misewu ndi nyumba akuluakulu mumzindawo.

“Nditangoona nkhope ya malemu ndidagwidwa ndichisoni ndipo ndidalephera kudzigwira koma kukhetsa msonzi.

Lachitatu pa 18, thupili adalitengera ku Mzuzu komwenso anthu adapereka ulemu wotsiriza mpaka Lachinayi.

Bob Pota yemwe ali mumzinda wa Mzuzu ndipo akuchita maphunziro aukachenjede a Community Development akuti sadzaiwala Mutharika pothetsa njala m’dziko muno.

Lachinayi cha m’ma 12 koloko masana thupiro limayembekezereka kunyamulidwa kupita ku Blantyre komwe anthu akuchigawo cha kum’mwera akapereke ulemu wotsiriza.

Thupilo likuyembekezeka kunyamuka lero kupita ku munda wa Mutharika wa Ndata m’boma la Thyolo ndikukalowa m’manda Lolemba pa 23.

Related Articles

Back to top button
Translate »