Amanga 10 pa mkangano wa ufumu
Apolisi ku Ntchisi amanga anthu 10 a m’mudzi mwa Kanyenda kwa T/A Kalumo potsatira mkangano wa ufumu pakati pa a Kanyenda ndi a Inje kwa zaka zitatu tsopano.
Yemwe adali mneneri wapolisi ya Ntchisi panthawiyo a Glory Kondowe adati anthuwo adagwidwa pa 27 November 2023 pa mkangano wa mbali ziwirizo omwe udagumulitsa nyumba ya a Inje.
“Pa mkanganowo nyumba ya Inje idagumulidwa komanso katundu wawo adabedwa koma apolisi atapitako anthu a m’mudzi mwa Kanyenda adawagenda,” adatero a Kondowe.
Iwo adati mkangano wa ufumuwo wakhala ulipo kwa zaka zitatu ndipo ngakhale mbalizo zimamenyana pafupipafupi, nkhani yawo ili kukhoti.
Anthu omwe agwidwawo ndi a Merifa Masache, Nazipeza Banda, Dulang’amba Mbewe, Paul Manuel, Dashani Kansalu, Alikeni Chiziro, Timoti Layifosi, Tsanzo Chichitike, Mickison Mangani ndi Kamtengo Jere.
“Apolisi atagendedwa adabwerera koma adakaonjezera mphamvu n’kupitanso mpomwe adakagwira anthu khumiwo ndipo akayankha milandu yonse yomwe akuzengedwa,” adatero a Kondowe.
Koma mneneri waunduna wamaboma ang’onoang’ono a Anjoya Mwanza adati mikangano ya ufumu nthawi zambiri imayamba chifukwa cha dyera.
Iwo adati ichi n’chifukwa chake undunawo uli ndi maganizo okhazikitsa mphala ya mafumu akuluakulu kuti iziunika ina mwa milandu yokhudza ufumu.
A Mwanza adapemphanso mabanja achifumu kuti azikhala ndi ndondomeko zabwino zokhudza ufumu wawo monga kusankhiratu munthu odzalowa ufumuwo ndikumvana chimodzi.
Nthawi zambiri mkangano wa ufumu umayambira pamaliro a mfumu ndipo pachifukwachi, boma lakhala likulimbikitsa mabanja achifumu kuti azisunga mbiri yaufumu wawo kupangira zamtsogolo.