Anatchereza

Ndikufuna kuchoka

Zikomo Anatchereza,

Ndidabwera kutauni kudzafuna ntchito ndipo ndidasiya mkazi wanga kumudzi. Ntchito ndidaipeza koma abale amene ndimakhala m’nyumba yawo akuti ndisachoke kukafuna nyumba ya lendi ati sakufuna mkazi wangayo abwere.

Kodi nditani kuti ndituluke m’nyumba yawoyo? Thandizeni.

Ine F.

Zikomo a F, ndinu mwamuna kotero pena sibwino kumvera zilizonse. Apapa zikuonetseratu kuti abale anuwo samufuna mkaziyo. Ngati mkaziyo ali ndi vuto ndibwino anene kuti vutolo mulikonze, koma kumuletsa si yankho. Achibale ena amafuna kulowerera chilichonse chokhudza moyo wa munthu, pena ndibwino kuti munthu azikhala ndi ufulu wosankha chomwe akufuna komanso kuchita. Musalolere, ngati pali vuto kambiranani.

Gogo,

Ndili ndi mwana wa kunjira ndipo ndidakwatira mkazi wa mwana kale. Koma iyeyo adabweretsa mwanayo ine ndidasakudziwa ndipo chichitire izi, sakundilabadiranso. Nditani?

Zikomo pa funso lanu lomveka. Choyamba ndifunse, kodi mayiwo adakuuzani kuti ali ndi mwana kunjira? Ngati sadakuuzeni ndiye kuti pali nkhani ziwiri, yoyamba imeneyo yachiwiri yoti abweretsa mwana mwa dzidzidzi. Bambo dziwani ichi kuti kholo lomwe aliyense amapanga zofuna zake silamoyo, kotero musalole kuti mpaka kude mutayambana ndi mkazi wanu. Mukhazikeni pansi ndipo akumasuleni nkhani yeniyeni. Ngati sakulankhula, kauzeni ankhoswe.

Anatchereza,

Ndili ndi zaka 28 ndipo ndili pabanja. Koma nthawi zonse ndikati ndikhale m’chikondi ndi mkazi wanga, amanena kuti watopa. Ndingatani.

M,

Lilongwe.

Zikomo bambo M,

Tikati banja timanena kuchipinda, ngati wina akukana kulowa kuchipinda ndiye kuti akukaniza banja. Mumufunse kuti kuchipindako akumalowako ndi ndani? Zikuonetseratu kuti pali tambala wina amene asangalala mwa mayiyo. Kodi zavuta? Auzeni ankhoswe ndipo amasule bwalo pamene pali vuto. n

Ndikufuna mwamuna

Ndine mayi wa zaka 52, ndimakhala ku Dedza. Mwamuna wanga adamwalira mu 2003. Ndikufuna mwamuna amene angandikwatire koma akhale wopemphera. Chonde imbani 0992256715.

Share This Post