ANATCHEZERA

Nditenge uti?

Anatchereza,

Munthune ndili ndi zibwenzi ziwiri. Zonsezi zidayamba chaka chimodzi panopa zatha zaka zitatu ndipo onsewa ndimawakonda chimodzimodzi inenso onsewa amandikondanso. Ndiye panopa ndapanga chiganizo chokhala ndi mmodzi. Ndipanga bwanji pamenapa?

Ine Zochenana

A Zochenana,

Akamati ichi chakoma ichi chakoma pusi anagwa chagada kapena kuti mapanga awiri avumbwitsa mumati akutanthauzanji? Ndi zimenezitu. Mwagwiratu njakata pamenepa chifukwa chosakhutitsidwa ndi bwenzi limodzi. Mwina mumayendera ija amati ‘have many but choose one’. Mphotho yosakhulupirika ndi imeneyo, achimwene. Ndanena kuti ndinu wosakhulupirika chifukwa kwa zaka zitatu mwakhala mukuyendetsa zibwenzi zanu pozinamiza kuti ‘ndiwe wekha’ pamene mulinso ndi wina amene mukumuuzanso kuti ‘ndiwe wekha’. Nanga tinganene kuti zibwenzizo zikudziwana ngati? Ndakaika kuti zikudziwana. Koma ndikuthokozeni kuti tsopano mwapanga chilinganizo choti mukhale ndi chibwenzi chimodzi. Izi ndiye zotamandika chifukwa mwaonetsa kukula. Kaya mukufuna kukwatira tsopano-ngati simunakwatire kale? Ndiye zikafika apa pamakhala matatalazi kusankha chifukwa mukuti onse mumawakonda chimodzimodzi. Koma mukunena zoona? Zingatheke zimenezo kukonda anthu awiri chimodzimodzi? Zimalephera olo ana ako obala wekha umatha kusiyanitsa chikondi ngakhale mwina suonetsera. Ndiye apa tangolimbani mtima, musankhe amene ali ndi makhalidwe oyenera kulowa naye m’banja. Penapake ayenera kusiyana ndithu. Palibe amene angakusankhireni, koma inu nokha, a Zochenana. Ndili ndi chikhulupiriro kuti simunapulupudze zoti mwina muli ndi ana ndi zibwenzizo. Apo ndiye zingakuvuteni kusankha koma ngati mudadzigwira sipangakhale vuto lenileni kusiyapo mmodzi. Zimachitika koma si mmene zimayenera kukhalira, abale.

Ndili pasukulu

Agogo,

Ndine mtsikana wa zaka 17 ndipo ndili pasukulu. Ndili ndi chibwenzi koma mnzangayo akuonetsa kuti sakukondwera nane ndiye ndimafuna kuti mundithandize maganizo kuti ndiziwerengerabe kapena ayi? Chonde ndithandizeni.

Iwe mtsikana,

Ukufuna ndikuthandize motani poti wanena kale kuti mnzakoyo akunetsa kuti sakukondwera nawe? Chomwe ndingakulangize n’choti zisiye za chibwenzizo ndipo ulimbikire sukulu. Sukulutu ndi yofunika kwambiri ndipo uike patsogolo, zina zonse pambuyo. Udakali mwana wamng’ono tsono zoyamba zibwenzi n’zachiyani? Sukulu ndi zibwenzi siziyenderana. Ngati ufuna kuti sukulu ikuyendere usamataye nthawi n’kuganiza za zibwenzi chifukwa mmalo moti uzimva zimene aphunzitsi akuphunzitsa uzingoganiza za bwenzi lakolo, osamva olo chimodzi, mapeto ake 0 pa 10! Atsikana ambiri sukulu imawakanika chifukwa cha nzeru ngati zakozo-kuika mtima pa zibwenzi. Kaya, zakozo! Usankhepo chimodzi ngati ufuna zako zikuyendere. Mwina bwenzi lakolo sakukondwera nawe chifukwa uli pasukulu ndiye akufuna usiye sukulu kuti uike mtima wako wonse pa iye. Koma ine ndikadakhala iweyo ndikadasankha sukulu, chibwenzi pambuyo.

Sakundipatsa ulemu

Ndine mwamuna wapabanja mkazi ndi wachiwiri koma sandipatsa ulemu chifukwa makolo ake ndi ochita bwino. Ndili naye mwana mmodzi. Kodi nditani kuti azindipatsa ulemu monga kale?

Achimwene,

Ulemu sachita kupempha! Umanena chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. Lero ndi lero basi mkazi wanu wayamba mwano, osakupatsani ulemu poti makolo ake ndi ochita bwino? Chilipochilipo chimene chimamupangitsa mkazi wanu kuti asakupatseni ulemu, osati chifukwa makolo ake ndi olemera. Mwina adayamba akuuzani kuti sangakupatseni ulemu chifukwa makolo ake ndi olemera? Ayi ndithu, munene chifukwa china, osati chimenecho. Mwanena nokha kuti poyamba ankakupatsani ulemu wonse, koma pano wasiya kutero, mukutanthauza kuti poyambapo makolo ake sadali ochita bwino? Koma simukunena bwinobwino ulemu umene mumafuna kuti mkazi wanu azikupatsani-azikugwadirani kapena aziti ‘wee bambo!’ mukamamuitana? Ulemu wake uti? Nkhanitu mukapanda kuilongosola inuyo bwinobwino kumakhalanso kovuta kuti munthu akuthandizeni zenizeni chifukwa simunaitambasule. Nditengerepo mwawi wopempha ena amene ali ndi mavuto ndipo akufuna kuti ndiwathandize kuti aziyala nkhani yawo bwinobwino, momveka kuti ndithe kumvetsa gwero la vuto lawo ndipo ndikatero nditha kupereka malangizo malinga ndi nkhani yawo mmene ilili.

OFUNA MABANJA

Ndine wa zaka 37 ndikufuna mkazi wa zaka kuyambira pa 40 mpaka 45. Wosangalatsidwa aimbe pa 0888 512 430

Ndili ndi zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi woti ndipange naye chibwenzi n’cholinga choti tidzakwatirane mtsogolomu. Akhale wa zaka za pakati pa 18-23, koma akhale wa ku Lilongwe.

Ndine mnyamata wa zaka 30 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 30 ndi 33 kuti ndipalane naye chibwenzi. Wotsimikiza aimbe pa 0888 904 690 kapena pa 0998 707 410.

Ndine mnyamata wa zaka 23ndikufuna mkazi wasiliyasai timange banja. Akhale woti sadaberekepo. SMS kapena kuimba pa 0884 859 821/0994 185 524.n

Share This Post