Anatchezera

Sitinakumanepo

Anatchereza,

Ndili ndi mkazi amene ndidamufunsira pafoni koma sitinaonanepo. Timangoimbirana foni basi koma amandiuza kuti amandikonda kwambiri. Ndimukhululupirire?

 

Zikomo,

Nzovuta kukuthandizani chifukwa simunanene kuti zidayamba bwanji kuti mumufunsire mkaziyo pafoni. Kodi nambala yake mudaitenga kuti? Adakupatsani ndi mbale wanu kapena mbale wamkaziyo? Mnzanu? Mnzake? Mwa njira iliyonse, nanunso mukuonetsa kuti mukhoza kukhala ndi kamtima ka chisembwere kapena mwalifunitsitsa banja ndiye mukufuna kupeza mkazi basi. Dekhani.

Komanso ine pokhala wa mvula zakale zambiri zikumandidutsa komabe adzukulu ena amandiuza kuti kunjaku kwadza njira zamakono zochezera pafoni monga Whatsapp, Facebook ndi zina zotere.

Sindikudziwa ngati nkotheka kuti mudapatsana manambala kupyolera m’njira zimenezi.

Choti mudziwe nchakuti njira zopezera mwamuna zimakhala zosiyanasiyana koma chachikulu chimakhala chakuti munthu amene ukumanga naye banja ayenera kukhala yekhayo ukumudziwa bwino.

 

Pali banja apa?

Zikomo gogo,

Tidamangitsa ukwati ndi mkazi mu 2010. Tili ndi mwana mmodzi. Ali ndi mimba, iye ankakana kukhalira malo amodzi ati poopa kuti mimba ichoka.

Nkhaniyo ndidaitengera kwa ankhoswe omwe adatithandiza kuti ziyambenso kuyenda monga banja. Koma mwanayo atabadwa, iye adayambanso kukana zokhalira malo amodzi ati chifukwa azikhala wotopa.

Nditayitengera nkhaniyo kwa ankhoswe, adayikanika.

Kuntchito adandisamutsira ku Mzuzu koma iye adakana kupita nawo. Ndidapitiriza kumulipirira lendi koma patatha miyezi ingapo adachoka ndipo adapita kwa mayi ake ku Blantyre.

Ndidapita komweko koma ukunso adakana zoti tikhalire malo amodzi. Ndichitenji?

NJ,

Zomba.

 

NJ,

Ndikudziwa kuti kukhalira pamodzi si ngodya yokhayo yomangira banja koma iyi ndi njira yosonyezera chikondi pa mwamuna ndi makzi wake choncho ngati wina apezeka kuti akulanga mnzake m’njira yotere, zimasonyeza kuti penapake zinthu si zili bwino.

Zifukwa zimene mkazi wanuyo akupereka ndi zopanda pake, kusonyeza kuti pali china chimene akubisa. Msinkhu wangawu, sindidamvepo kuti mimba yachoka chifukwa mwamuna ndi mkazi amagonana mkaziyo ali woyembekezera ndiye izi akuzitenga kuti?

Komanso mudziwe kuti mkazi wanuyo akudziwa kuti apa banja lathapo basi. Poyamba, kukukanizaniko. Kachiwiri, nchifukwa chiyani adakana kukutsatirani kuntchito? Ndipo pomaliza nchifukwa chiyani wabwerera pakhomo la amake? Zonsezo ndi zizindikiro kuti apa paipa.

Chofunika nchakuti mupite kwa ankhoswe mukatule nkhaniyi.

 

Adasintha

Gogo,

Ndili ndi mkazi yemwe ndili naye mwana wa zaka zitatu. Malinga ndi mavuto a zachuma, ndidachoka ku Blantyre kudzagwira ntchito ku Lilongwe. Patatha miyezi ingapo adanditsatira.

Koma chongobwera kuno, iye adasintha ndipo amakonda kucheza ndi amayi oyendayenda.

Ndichitenji?

M, Lilongwe.

M,

Poyamba simunandiuze ngati ukwati wanu uli wa kwa ankhoswe kapena mudangotengana. Ngati ndi wa ankhoswe, kawakambireni.

Ngati ayi, poyamba muyenera kumufunsa mkazi wanu chifukwa chimene akuyendera ndi amayi oyendayendawo. Mumuuze kuti ayenera kusintha ndipo ngati sasintha, chochita mukuchidziwa kale. Kunjaku kwaopsa adzakubweretserani matenda.

 

OFUNA MABANJA

Ndili ndi zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndimafuna mwamuna wa chi Rasta. Osangalatsidwa aimbe pa 0881838385

 

Ndikufuna mkazi. Ndichitenji kuti ndimupeze. 0885655108

 

Share This Post