Anthu 49 afa ndi mphenzi
Mphezi zavuta chaka chino. Pofika lero anthu 49 aphedwa ndi mphenzi chiyambireni nyengo ya mvula, poyerekeza ndi 32 omwe adafa ataombedwa ndi mphenzi chaka chatha, malinga ndi chiwerengero chochokera ku nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi.
Mwa anthuwa, oposa 10, adamenyedwa ndi mphenzi ali mkati mwa nyumba kapena tchalitchi.
Masiku apitawo, banja lina lamwalira litamenyedwa ndi mphenzi m’boma la Kasungu. Banjalo lidali mtulo panthawi ya ngoziyo.
Austin Bosco wa zaka 52 pamodzi ndi mkazi wake Anesi Banda wa zaka 32 adamenyedwa ndi mphenziyo usiku wa Loweruka. Mneneri wapolisi m’boma la Kasungu Miracle Mkonzi adatsimikiza za ngoziyi.
Aka si koyamba anthu kumwalira ndi mphenzi ali m’nyumba zawo chifukwa sabata zapitazo, amayi ena 5 adamwaliranso atamenyedwa ndi mphenzi m’tchalitchi m’boma la Chitipa pomwe mnyamata wina adamwaliranso m’boma la Nkhata Bay atamenyedwa ndi mphezi ali m’nyumbanso.
Izitu zikuchitika ngakhale a za nyengo amanena mobwerezabwereza kuti anthu azikhala m’nyumba mvula ikamavumbwa.
Polankhulapo, mkulu wa nthambi yoona za nyengo m’dziko muno Jolamu Nkhokwe adati vuto ndi nyumba zomwe zikumangidwa m’dziko muno.
“Ziphaliwali komanso mphenzi zikuchulukira chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Ndipo mphenzizi zikumamenya ndi anthu omwe ali m’nyumba omwe chifukwa choti nyumba zathu timamanga osafikira mlingo wina omwe ngoika zitsulo zomwa mphenzi,” adalongosola motero Nkhokwe.
Iye adati pomanga nyumba, n’kofunika kumaika zitsulo zomwe zimamwa mphenzi kuti zikamenya nyumba, mphamvu ya magetsi ake isamalowe m’nyumba koma izipita pansi mothandizidwa ndi zitsulozo.
Malinga ndi Nkhokwe, nyumba zambiri za pulani komanso sukulu zambiri m’dziko muno zili ndi mawaya kapena zitsulo zomwa mphenzizi.
“Koma nyumba zathu zambirizi, zilibe waya ameneyu ndipo ichi n’chifukwa chake tikumva kuti mphenzi zikuomba anthu ngakhale ali m’nyumba kapena m’tchalitchi,” adatero Nkhokwe.
Ndipo apa katswiri wa zanyengoyi adalangiza anthu kuti pomanga nyumba, aziyesetsa kuika zitsulozi popewa kumenyedwa ndi mphenzi.
Iye adapemphanso nthambi za boma zoona za mamangidwe kuti zizilengeza kwa anthu ndondomeko zoyenera kutsata pomanga nyumba zawo.