Anthu ochuluka akufuna katemera
Pomwe zipatala zambiri zayamba kubaya katemera woteteza ku matenda a Corona mu gawo loyamba, achipatala ati anthu ankhaninkhani omwe sali nawo mu gawo loyambali akuonetsa chidwi chofuna kubayitsa.
Msangulutso udayankhula ndi aneneri a za umoyo ku mpoto m’boma la mzimba, ku Blantyre komanso ku Lilongwe ndipo onsewa adati akulandira anthu ambiri ofuna kulandira katemera ngakhale sali nawo mu gawo loyambali lomwe ndi la ogwira ntchito za umoyo komanso zachitetezo.
Polankhulapo mneneri wa ofesi ya za umoyo ku mppoto m’boma la Mzimba Lovemore Kawayi adati katemerayu akuyenda bwino ndipo akulandira anthu ambiri omwe sali nawo m’gawo loyamba.
“Anthuwa tikumawabweza powauza kuti nthawi yawo yolandira katemera ikadzakwana tidzawalengeza,” adalongosola Kawayi.
Iye adati ofesi yake sidalandire dandaulo lililonse kuchokera kwa anthu omwe alandira katemerayu kupatula kuphwanya m’thupi ndi litsipa zomwe zimachitika ndi katemera aliyense.
Pofika Lachiwiri, anthu 477 adali atabayitsa m’boma la Mzimba.
Ndipo wofalitsa uthenga wa za umoyo ku Blantyre, Wongani Mbale, adati ofesi yake ikulandira anthu ambiri ochita bizinesi omwe akufuna kulandira katemera.
“Koma anthuwa tikumayetsetsa kuwalongosolera kuti nthawi yawo sinakwane ndipo akumamvetsetsa,” adalongosola Mbale.
Iye adati anthu ambiri a m’gawo loyamba amulandira bwino katemerayu chiyambireni kulandiritsa Lolemba lapitali.
Malinga ndi Mbale, ofesi yake pofika Lachitatu, idali itapereka katemera kwa anthu 1 375.
Malinga ndi mneneri wa zaumoyo m’boma la Lilongwe, Richard Mvula anthu ofuna kulandira katemera akuchulukira ndi m’magulu a anthu omwe ali ndi matenda amgonamgona komanso omwe ali ndi zaka zopitirira 60.
“Tikungowapempha kuti adikire nthawi yawo,” adalongosola Mbale.
Malinga ndi nduna ya zaumoyo, Khumbize Chiponda, anthu 9 091 ndi omwe adali atalandira kale katemerayu pofika Lachinayi.
Iye adati gawo lachiwiri la katemerayu ndi la anthu omwe ali ndi zaka zopitirira 60, omwe ali ndi matenda amgonamgona komanso a ntchito zina monga zautolankhani.
Pofika pa March 16, anthu 32 894 ndiwo adwala matenda a Corona m’dziko muno pomwe anthu 1 088 adamwalira ndi matendawa.
Mwa anthuwa, 26 890 adachira ku matendawa kuyimira 81.8 peresenti.