Anthu sakudziteteza ku matenda a Covid-19
Ngakhale akadaulo azaumoyo adalosera kuti chiwerengero cha odwala Covid-19 chikwera kwambiri mwezi uno, anthu ambiri sakutsata njira zodzitetezera ku matendawa.
Kafukufuku yemwe Tamvani yachita waonetsa kuti anthu ambiri akukhalabe atatuatatu kapena anayianayi pa mpando m’minibasi, komanso njira zodzitetezera sizikutsatidwa m’misika, m’maliro, m’malo azisangalalo ndi ena.
Akadaulo azaumoyo, mlembi wa bungwe la Minibus Owners Association of Malawi (Moam) Coxley Kamange, komanso mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera atsimikiza za vutoli.
Maziko Matemba, mmodzi mwa akadaulo azaumoyo, adati ndi wokhumudwa kaamba koti anthu ambiri sakutsatira njira zodzitetezera ku Covid-19 zomwe zikuchititsa kuti chiwerengero cha anthu opezeka, komanso kumwalira ndi matendawa chizikwerabe.
Iye adati izi zikuchitika kaamba ka zinthu ziwiri.
“Choyamba ndi mbiri ya Covid-19. M’mbuyomu anthu amati Covid-19 ili m’maiko ena, koma m’dziko muno siidafike.
“Chachiwiri ndi choti boma, komanso nthawi ya zaumoyo siikukakamiza anthu kutsatira njira zodzitetezera,” iye adatero.
Koma woimira boma pa milandu, Chikosa Silungwe, adati n’kovuta boma kukakamiza anthu kutsatira ndondomeko zodziteteza kaamba ka ziletso zomwe amipingo, komanso bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) adatenga ku khoti motsutsana ndi ndondomekozo.
“Monga mukudziwa pali ziletso pa nkhani ya ndondomeko zopewera Covid-19. Choncho n’kovuta kukakamiza munthu kutsatira ndondomekozo chifukwa kutero kukhala ngati kuderera khoti,” adatero Silungwe m’chikalata chomwe adalembera boma m’mbuyomu.
Kadadzera akugwirizana ndi Silungwe kuti manja aapolisi ndi omangidwa chifukwa cha ziletsozo.
“Monga mukudziwa boma lidatulutsa ndondomeko zopewera Covid-19, koma mabungwe, amipingo ndi ena malo azisangalalo adakatenga ziletso. Choncho n’kovuta apolisi kuchitapo kanthu,” adatero Kadadzera.
Iye adati apolisi akamachititsa misonkhano yachitetezo m’midzi akumauza anthu zaubwino wotsatira ndondomekozo.
Wothandizira mkulu woyang’anira apolisi a pa msewu, Mcferson Matowe, adati boma lidakhazikitsa lamulo loti mibasi zizinyamula anthu awiriawiri pa mpando osati atatu kapena anayi.
Mchitidwe wotenga anthu opyolera muyezo pa mpando ukumachitika anthu akaweruka ku ntchito madzuro.
Daniel Renato, mmodzi mwa okwera minibasi mu mzinda wa Blantyre, adati anthu akukwerabe minibasizo kaamba koti mitengo yake ndi yotsika poyerekeza ndi zokwera awiriawiri pa mpando.
“Ngakhale mitengo ya mafuta idatsika, eni minibasi sadatsitse mokwanira mtengo wa minibasi kuti anthu azitha kufikira,” adatero Renato.
Matowe adali padakali pano n’kovuta kuti apolisi apa msewu azipezeka paliponse chifukwa ndi ochepa, komanso kugwira ntchito usiku pofuna kuthana ndi mchitidwewu.
Kamange adati apempha eni minibasi kuti azipereka mankhwala wophera tizolombo (sanitizer) kwa okwera minibasi kuti azipaka m’manja, komanso kuonetsetsa kuti aliyense wokwera minibasi wavala zotchinga kukamwa ndi kumphuno.
George Jobe, kadaulo wa zaumoyo, adati n’zomvetsa chisoni kuti anthu akunyozera ndondomeko zopewera Covid-19 m’malo osiyanasiyana.
“Ndondomeko zomwe zidatsatidwa kwathunthu ndi kutseka malo ena ogwira ntchito, mabwalo a ndege ndi sukulu,” adatero Jobe.
Malinga ndi unduna wa zaumoyo, chiwerengero cha anthu odwala Covid-19 chidafika pa 4 426 pamene cha omwalira chinali pa 136 Lachitatu sabata ino.