Nkhani

Aonjezera aphungu

Listen to this article

Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latsutsa mphekesera yoti layamba laimika kaye chilinganizo choonjezera madera a aphungu pa chisankho cha chaka cha mawa.

Pa 18 November 2022, aphungu a Nyumba ya Malamulo adavomereza pempho la MEC kuti chiwerengero cha aphungu chikwere kuchoka pa 193 kufika pa 229 pomwe cha makhansala chichoke pa 462 kufika pa 509. MEC idati idachita izi potsatira lamulo limene limapereka mphamvu yotero ku bungwelo.

MEC idati kuonjezerako kudachitika chifukwa nthambi yoona za zowerengera zosiyanasiyana m’dziko muno la National Statistical Office lidati pofika 2025 kudzakhala anthu 10 957 490 amene akuyembekezeka kudzaponya voti chaka cha mawa.

M’chikalata chimene adasainira mkulu wa zisankho a Andrew Mpesi, mphekesera yoti bungwe lawo silionjezera chiwerengero cha aphungu ndi makhansala ndi yabodza.

“Zoti sitisintha chiwerengero cha aphungu mopemphedwa ndi a banki yaikulu ya IMF ndi zabodza. Kusintha malire sikumangochitika mwa ife tokha ngati a MEC chifukwa timafunsa onse okhudzidwa mosabisa kanthu. Izi tikuchita potsatira malamulo a zisankho komanso malamulo aakulu a dziko lino,” adatero a Mpesi.

Iwo adati potsatira malamulowo, kusintha kwina kudzachitika m’chaka cha 2032 ndipo adapempha Amalawi kuti azidekha asanafalitse nkhani zosatsimikizika.

Kusintha komaliza madera a aphungu kudachitika m’chaka cha 1999 pomwe chiwerengero cha aphungu chidakwera kuchoka pa 177 kufika pa 193. Malinga ndi kusinthaku, m’chigawo cha kumpoto tsopano mukhala aphungu 38 kuchoka pa 33, pakati pakhala 93 kuchoka pa 73 ndipo kumwera kukhala aphungu 98 kuchoka pa 87.

A Yusuf Mwawa omwe ndi wofalitsa nkhani za chipani cha UDF adati chipanicho ndi chokhutira ndi kuchulukitsa kwa madera a aphungu chifukwa ndimo lamulo limanenera pakakhala kofunika kutero.

“Lamulo lili ndi mphamvu ndipo ngati wina akufuna kuletsa zokuza madera a aphungu, ayenera kuchotsa lamulolo. Tamva kuti ena akufuna kuti chiwerengero cha aphungu chisakwere, koma ife maganizo athu tidawapereka kale ku MEC atatipeza,” adatero iwo.

Mneneri wa chipani cha Malawi Congress Party a Ezekiel Ching’oma ati sanganeneretu ngati akugwirizana ndi zochulukitsa chiwerengero cha aphungu kapena ayi.

“Tachivomereza chifukwa malamulo a dziko lino amaneneratu kuti bungwelo liyenera kuonjezera chiwerengero cha aphungu ngati pakufunika kutero. Izi amachita potengera kuchuluka kwa anthu.

“Madera ena a aphungu amakhala a anthu ochuluka kwambiri choncho amayenera agawidwe ndithu. A MEC adatipeza ndi kumva maganizo athu asanagawenso malirewo. Izi zidachitika kudera, paboma komanso dziko lonse,” adatero a Ching’oma.

Iwo adaonjeza kuti n’zoona kuti kuchulukitsa chiwerengero cha aphungu kuchititsa kuti ndalama zambiri zilowepo.

“Ulamuliro wa demokalase siotchipa. Kugawanso madera a aphungu kuthandiza kuti Amalawi m’maderawa azilandira zitukuko mofanana,” adatero a Ching’oma.

Koma mneneri wa chipani cha UTM a Felix Njawala adati polingalira za momwe chuma cha dziko lino chikuyendera, kuchulukitsa chiwerengero cha aphungu kukadaima kaye.

“Ngakhale a MEC adafunsa anthu maganizo awo, amayeneranso kuunikira nkhani ya zachuma poyerekeza ndi momwe Amalawi angapindulire ndi kuchulukitsa chiwerengero cha aphungu. N’chachidziwikire kuti kuonjezera chiwerengero cha aphungu kuchititsa kuti ndalama zimene zimalowa ku CDF zichuluke,” adatero a Njawala.

Malinga ndi kuwerengera kwathu, kuonjezera chiwerengero cha aphungu kuchititsa kuti ndalama za CDF zikwere kuchokera pa K1.93 biliyoni kufika pa K2.29 biliyoni pa mwezi.

Related Articles

One Comment

Back to top button
Translate »