Nkhani

Apereka ambulansi ku Bangwe

Katika: Yatha miyezi iwiri
Katika: Yatha miyezi iwiri

Kwa kanthawi anthu makamaka amayi oyembekezera akhala akuvutika mayendedwe popita ku chipatala cha Bangwe Clinic mumzinda wa Blantyre. Anthu omwe amavutikawa ndi omwe akukhala ku Mpingwe ndi Mvula chifukwa kumaloko sikufika ma minibasi kaamba koipa kwa msewu.

Pano mavutowa tsono angakhale mbiri yakale pomwe anthuwa alandira minibasi komanso ambulance yomwe idziyenda kumeneko. Zinthuzi zaperekedwa ndi yemwe amakonza masewero a nkhonya komanso amiyendo Justice Katika.

“Ndikulankhula pano ambulansi yatha miyezi iwiri ikugwira ntchito pomwe bus yaperekedwa kumene. Anthu akumeneko akhala akundipempha thandizo malinga ndi mavuto omwe akukumana nawo ndiye ndachita malinga ndi pempho lawo,” adatero Katika m’sabatayi

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button