Nkhani

Zaka 6 chifukwa choononga njanji

Bwalo la milandu la Second Grade Magistrate m’boma la Dowa lagamula a Laurent Chigowa, a zaka 45 kuti akakhale ku ndende kwa zaka 6 chifukwa choononga njanji ya sitima yomwe imakonzedwa kupita ku Kanengo m’boma la Lilongwe.

Woimira boma pa milandu, a Superintendent Ian Ntaba, adauza khotilo kuti pa 18 September polisi ya ku Chezi idalandira dandaulo kuchokera ku kampani yoyendetsa maulendo a sitima za pa mtunda la Cear, kuti zipangizo zawo zina zidabedwa komanso kuonongedwa.

Mmodzi mwa alonda adauza apolisiwo kuti iwo adapeza pa khomo pena pali zinthu zina zopangidwa kuchokera ku zipangizo za njanji. Ndipo dengu lomwe lidakonzedwalo linaikidwa pa shopu yomwe amaotchererapo zitsulo zosiyanasiyana pa msika wa Chankhungu m’bomalo.

“Kutsatira kafukufuku amene achitetezo adachita, apolisi adamanga mwini shopuyo yemwenso anaulula kuti adagula zipangizozo kuchokera kwa bambo Chigowa. Choncho, apolisiwo adapita kwa bamboyo kukam’manga komanso kukatenga zipangizo za njanji zina zomwe anasunga, zomwenso ndalama zake ndi K7.2 miliyoni,” iwo adatero.

Atafunsidwa ndi apolisiwo, a Chigowa adavomera kuti ndi iwo amaba ndikuononga zipangizo za njanjizo ndipo akhala akuchita izi kwa nthawi yaitali, zomwe iwo amakagulitsa kwa anthu opanga katundu wa zitsulo.

Atakaonekera kubwalo la milandu, a Chigowa adayamba ndikuukana mlanduwo koma kenaka adauvomera. Ndipo khotilo lidamupeza wolakwa mkuluyo poononga njanjiyo motsutsana ndi Gawo 344 (1) lomwe limawerengedwa ndi Gawo 344 (6) la malamulo a dziko lino.

Ndipo mkuluyo adapepesa kwa akuluakulu a kampaniyo napempha kuti akhoti amukhululukire ati chifukwa ali ndi banja lomwe limadalira iye komanso amathandiza ana ake ena omwe ali ku sukulu za ukachenjede.

Koma Superintendent Ntaba adapempha khotilo kuti lipereke chilango chokhwima kuti likhale phunziro pa mchitidwe woyipa womwe wakhala akuchitawo.

Popereka chigamulo, woweruza mlanduyo a Chifundo Matchaya, adagamula mkuluyo kuti akakhale kundende kwa zaka 6.

A Chigowa amachokera m’mudzi mwa Ntungwi, m’dera la T/A Chiwere m’boma la Dowa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button