Nkhani

Kuteteza chilengedwe

Pomwe vuto la mapulasitiki opyapyala likupitirira kuononga chilengedwe, ophunzira awiri a pa sukulu ya ukachenjede ya Mubas adza ndi mapulasitiki opyapyala omwe aziola komanso ziweto zikhonza kudya.

Ngakhale bwalo la milandu lalikulu m’dziko lino lidagamula kuti mapulasitikiwa ndi oletsedwa m’dziko lino, iwowa akupitirira kupezeka m’misika. Kaamba koti siamaola, mapepalawa amaipitsa dziko, kuchititsa kuti nthaka iguge, kuononga miyoyo ya za m’madzi komanso ziweto zikadya zimafa.

Koma Marcus Mulwa ndi Lonass Kapira omwe amaphunzira phunziro la sayansi lotchedwa chemistry adza ndi pulasitiki loolali ndiponso akulikonza m’magawo awiri: Lina loti anthu akhonza kudya ndi lina loti ziweto zikhonza kudya.

Mphunzitsi wa chemistry ndi zosamalira chilengedwe ku Mubas Mayi Gladys Chimwemwe Banda adati ndi okondwa ndi luntha la achinyamatawa ndipo ali ndi chikhulupiriro chonse kuti ngakhale izi zidali gawo la maphunziro awo, akhoza kuzitengera patali ndi kupeza kampani yoti izikonza mapulasitikiwa mochuluka.

“Pulasitiki akonzali likhonza kuthandiza kwambiri kuthana ndi mavuto a kuonongeka kwa chilengedwe. Ndikukhulupirira kuti iwowa akalembetsa zimene apangazi ku boma kuti wina asawabere luso lawoli,” adatero a Chimwemwe Banda.

Mawu ake, Lonass adati ali ndi chiyembekezo chonse kuti akufuna kwabwino awathandiza kuti luntha lawoli alitengere patali. Iye adati amagwiritsa ntchito sitalichi wa mbatata ndi madeya a chimanga pokonza mapulasitikiwa.

“Maloto anga ndinkafuna kukaphunzira Social Sciences ku sukulu yya ukachenjede ya Unima koma nditabwera kudzaphunzira sayansi ndidadziwa kuti ndiyenera kuikapo mtima ndipo ndine wokondwa kuti tadza ndi luntha lotere. Pali magawo awiri: Gawo lina anthu akhoza kudya mapulasitikiwa, osataya pomwe gawo lina ziweto zikhonza kudya osafa,” adatero iye

Marcus adati akufuna kudzakhala katswiri wa sayansi wodziwika pa dziko lonse makamaka posamalira za chilengedwe ndi kukonza zinthu zatsopano m’njira ya sayansi.

Iye adati: “Ndikufuna kudzathandiza achinyamata kuchilimika pa nkhani ya sayansi ndi kukonza zinthu zosaononga za chilengedwe.”

Malinga ndi mmodzi mwa omenyera zoteteza chilengedwe a Matthews Malata, luntha la achinyamatalo ndi la pamwamba koma adapempha mabungwe, boma ndi makampani kuti atukule achinyamata otere.

“Achinyamata m’sukulu za ukachenjede akubwera ndi luso la pamwamba koma sizipita patali, zimangothera ku sukulu. Ena ayenera kuchitapo kanthu kuti zimene akupangazi zizipangidwa zochuluka ndi makampani. Choncho dziko lidzapita patsogolo,” atero iwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button