Nkhani

Apezeka ndi foni m’mimba

Nthambi ya zandende m’dziko muno yaimika kaye pantchito woyang’anira ndende Emmanuel Chiganda, yemwe mkaidi amene adapezeka ndi foni ziwiri m’mimba adamutchula kuti akukhodzidwa.

Mneneri wa nthambiyo a Chimwemwe Shawa adatsimikiza izi Lachisanu

Foni kundende monga ya Zomba n’zoletsedwa

Mkaidiyo, a Frank Siposi, adadabwitsa anthu pomwe adapezeka ndi fonizo m’mimba ndipo adagonekedwa pachipatala cha Zomba. Iye adatuluka m’chipatala Lachisanu.

“A Chiganda Lachitatu adakaonekera kubwalo losungitsa mwambo kuntchito za ndende. Apa awaimika kaye ntchito pomwe zofufuza zikadali mkati koma umboni ukapezeka akhonza kuchotsedwa ntchito chifukwa zidachitikazi n’zolakwira malamulo oyendetsera ndende za dziko lino.

“Akangopezeka wolakwa ndiye kuti nkhani ikafika kwa woyang’anira ndende m’dziko muno, kuchoka apo ikafika kwa omwe amalemba ndi kuchotsa anthu ntchito kundende ndipo ndi omwe atadzakhale ndi chigamulo chomaliza,” anatero a Shaba.

Iwo adati a Chiganda agwira ntchito m’ndende kwa zaka 19. Adaonjeza kuti nkhaniyi ili apo, nthambiyo yaimikanso a Josophat Mphangwe ndi a Rashid Kamwendo a kundende ya Lilongwe (imene imatchuka kuti Maula) powaganizira kuti amalowetsa chamba m’ndendeyo.

A Siposi adamangidwa pa 16 September 2011 pamlandu woti adathyola nyumba ndi kuba njinga ndipo adagamulidwa kukaseweza kwa zaka 19. A Shawa adati malinga ndi kuwerengera kwa andende, iwo amayenera kutuluka pa 15 July 2023.

“Apa iyeyo adapalamula mlandu wolowetsa katundu woletsedwa kundende umene akuyenera kuzengedwa,” adatero a Shawa.

Dotolo wamkulu pachipatala cha Zomba a Saulos Nyirenda adatsimikiza kuti a Siposi adapezeka ndi foni ziwiri m’matumbo ake.

Malinga ndi iwo, mkaidiyo adachita chimbudzi kuti fonizo zituluke.

Siposi adati mmodzi mwa ogwira ntchito kundendeyo adawalemba maina kukalambula ndipo ataweruka, akaidi ena adauzidwa kukalowa mkati pomwe anayi adawatenga kupita kunyumba kwawo. Atafika uku, adawapatsa foni ziwiri.

Iwo adati atachoka uku, adapita kudimba kokathirira mbewu ndipo atamaliza ndi pomwe adalongeza fonizi m’matumbo ake.

“Adati imodzi mwa fonizi ndikamupatse m’kaidi wina, anamubweretsera ndi mkazi wake pomwe inayo adati ndigulitse pa mtengo wa K40 000. Koma nditafika mkati sindinapereke chifukwa zidali m’mimba zimakanika kuchoka,” adatero a Siposi.

Iwo adati yemwe amawalonderayo ndiye adamupatsa nzeru zopaka mafuta a mtedza pafoni zamtundu wa Itel-zo ndi kulowetsa kumalo omwe amatulutsira chimbudzi.

Kwa nthawi yaitali m’dziko muno, Amalawi akhala akudandaula kuti akuberedwa ndalama za nkhaninkhani ndi akaidi a ndende za Maula, Zomba komanso Chichiri omwe amapezeka ndi foni za m’manja.

Mwezi wa February chaka chino gadi winanso wochokera ku ndende ya Chichiri anagwidwa atamuthandizira mkaidi kuba K326 000 za wapolisi wina mumzinda omwewo wa Blantyre.

Ndipo akampani ya foni ya TNM, chaka chatha anadandaulapo kuti akaidi ochokera ndende ya Zomba ndiwo akubera kwambiri anthu pafoni.

Mkulu wa kampaniyo Arnold Mbwana anauza aphungu ena a Nyumba ya Malamulo kuti 91 mwa anthu 100 omwe akuberedwa pafoni, nkhani zake zikuchokera kundende ya Zomba ndipo ikukhudza alonda a ndende ndi akaidi.

Lachitatu, wapampando wa bungwe loyendera ndende la Malawi Inspectorate of Prisons a Kennan Manda anati foni 450 zinalandidwa kundende ya Zomba kumayambiriro a chaka chino.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button