Mlandu wa a Malemia ukupitirira mawali
Bwalo la milandu la Zomba Senior Resident Magistrates Court kuyambira 8 koloko mawa lino lipitiriza kumva mlandu wa a Senior Chief Malemia omwe akuwaganizira kuti adagona ndi mtsikana wa zaka 16 n’kumupatsa mimba kenako n’kumuchotsetsa.
Izi ndi malingana ndi zikalata za bwalo zimene taona zimene zikusonyeza kuti mlanduwo akufuna kuti uyende mwachangu, kaamba koti woganiziridwawo sadatulutsidwe pa belo.

Malinga ndi zikalatazo, bwalo likufuna kumalizitsa kumva umboni ngakhale lero ndi mawa lomwe ndi tsiku la tchuti mpaka mkuja.
Izi zikudza pomwe woweruza mlanduwo a Elijah Daniels Lachitatu sabata yatha adauimika kaye chifukwa choti pomwe woimira mfumuyo pa milandu a Patrick Debwe amafunsa mayi a mwanayo mafunso atapereka umboni wawo nthawi yoweruka ya boma 4:30pm idali itakwana ndipo bwalolo lidaonjezera nthawi mpaka 5pm.
Koma a Debwe, omwe amagwira ku kampani ya Chimowa and Associates Law Consultants, adali asadamalize kotero bwalolo lidaimitsidwa kuti adzapitiriza kufunsa mayiwo pa tsiku loikikalo.
Mfumuyo, yomwe dzina la pa msonkho ndi a Lloyd Clement ndipo ali ndi zaka 33, itaonekera ku khotilo Lachitatu, mtsikanayo adaperekera umboniwo m’kachipinda komata kaamba koti ayenera kutetezedwa pokhala wachichepere.
Ndipo popereka umboni wawo, mayi a mtsikanayo amene ndi a zaka 50, adati adayamba kumukaikira mwezi wa December chaka chatha kuti adali ndi mimba koma akamufunsa amakana.
Iwo adati chifukwa amakhala pafupi ndi a mfumu woganiziridwawo, adakawauza akazi awo kuti awathandizire kufunsa mwanayo ngati ali ndi mimba kapena ayi. Atamufunsa adavomera.
“Koma atamufunsa kuti mimbayo adamupatsa ndani, adayankha kuti zimenezo zisawakhudze. Mmawa wa pa 26 February mtsikanayo adayamba kuonetsa zizindikiro zoti akudwala koma pomufunsa, adakana,” adatero iwo.
Malinga ndi mayiwo, adapitanso kwa mkazi wa mfumuyo kukawauza zizindikiro zimene mtsikanayo amaonetsa. Iwo adati mayi mfumuwo adati dzulo lake adamuona akukwera minibasi atanyamula ka chikwama kakang’ono.
Mayiyo atabwerera ku nyumba kwawo, adati adapeza mtsikanayo ali mu ululu ndipo atatsegula kachikwamako adapeza kapaketi ka mankhwala koma mulibemo mapilitsi. Ndipo adapezamonso lisiti lomwe adagulira mankhwalawo.
“M’ma 2 koloko masana, matenda adakulirabe ndipo adawauzanso akazi awo a mfumuwo awaperekeze ku chipatala cha St Lukes m’bomalo. Madokotala atamufunsa adayankha kuti adamwadi mankhwalawo m’ma 8 koloko mmawa ndipo atamufunsa kuti mankhwalawo adawatenga kuti adayankha kuti kwa chibwezi chake,” adatero mayiyo.
Ndipo adapitiriza kuti madotolowo adawafunsanso ngati mtsikanayo adali atayamba kale sikelo. Pakati pa usiku, mtsikanayo adabereka senye.
Mayiyo adapereka ku bwalolo ka bokosi ka mankhwalako ndi lisitiyo ngati umboni.
Mayiwo atamaliza kupereka umboni wawo, a Debwe adafunsa mayiwo kuti ngati munthu amene wakhala akubereka kwa nthawi yaitali n’chifukwa chiyani zidawatengera nthawi yaitali kuzindikira mimbayo mu December osati miyezi yoyambirira ya mimbayo?
Ndipo mayiwo adayankha kuti kuonekera kwa mimba kumatengera thupi la munthu. Iwo adapereka chitsanzo choti amayi ena amatha kutenga mimba koma kumasambabe (menstruation).
Ndipo adaonjezera kuti pokhala mimba yoyamba, ena imatha kuonekera mwachangu pamene ena siamaonekera ngati mmene zidalili ndi mtsikanayo.
Popereka umboni wawo, bambo a mwanayo omwe ali ndi zaka 56 adati ali ndi ana 7 ndipo mwanayo adabadwira pa chipatala cha Naisi ku Zomba pa 29 June 2009.
Iwo adatinso adatumiza uthenga wa WhatsApp kwa amfumuwo ndi kuwafunsa zomwe amadziwa za pathupi ndi kuchotsa mimbako.
Bambowo adati amfumuwo adati ali ku Salima ndipo mawa lake pa 28 February adawauza kuti abwerako ndipo adawapempha kuti akumane kwa Jokala.
“Titakumana, amfumuwo adapepesa kaamba kogona ndi mwana wanga, kumupatsa mimba ndi kumuchotsetsa. Amfumu adandiuza kuti azimuthandiza ngakhale kumulipirira sukulu koma ndidakana ndi kuwafunsa kuti akadakhala mwana wawo akadatani?” adatero bambowo.
Iwo adapitiriza kuti adauza mfumuyo kuti mwanayo akatuluka ku chipatala, ndalama zonse adzalipira ndi iwowo, zimene a mfumu adavomera.
Mtsikanayo adatuluka ku chipatala pa 3 March ndipo adawauza kuti ndalama zolipira ku chipatalako zidakwana K114 000 ndipo iwo adatumiza ndalamayo.
Pa 17 March, bambowo adalandira uthenga pa WhatsApp kuwafunsa kuti adakasiya nkhaniyo ku polisi ndani koma iwo sadayankhe. Iwo adauza bwalo kuti amfumuwo adawapempha kuti akanene kuti mtsikanayo ndi wa zaka 18 ndipo sadayankhenso.
Iwo adapereka mauthenga a WhatsApp ngati umboni wawo.
Pofunsa bambowo pa umboniwo, a Debwe adati ndi chifukwa chiyani mfumu imene ndi yolemekezeka amaifunsa nkhaniyo kudzera pa WhatsApp osadzera kwa nduna kapena alangizi a mfumuwo?
Bambowo adati nthawi zambiri mayankhula nawo pa WhatsApp kaamba koti iwonso ndi mmodzi mwa atsogoleri a za nkhalango ku deralo
A Debwe adafunsanso bambowo chifukwa chomwe chidachititsa kuti atenge nthawi asanazindikire pathupi pa mtsikanayo ndipo adayankha kuti nthawi zambiri amakhala ali ku ntchito ndipo akaweruka amapeza mwanayo akuchita za ku sukulu.
Woimira Senior Chief Malemiawo adafunsanso bambowo ngati akudziwa anzake onse a mtsikanayo ndipo adayankha kuti akudziwa atsikana okhaokha. Ndipo atawafunsa kuti sukulu akuphunzira mtsikanayo ndi ya amuna ndi akazi sakuganiza kuti mtsikanayo ali ndi amnzake ena amuna ndipo abambowo adati sakudziwa.
A Debwe adafunsanso bambowo ngati adachitapo maphunziro a za chipatala ndipo bambowo adati ayi.
A Lloyd Clement ndi a zaka 33 ndipo amachokera m’mudzi mwa Malemia ku Zomba.
Woimira boma pa mlanduwo, ndi mayi Josephine Chigawa ndipo ukupitirira.



