Nkhani

Aphungu akwangula zokambirana

Listen to this article

Pamene aphungu a Nyumba ya Malamulo amayembekezeka kukwangula zokambirana zawo dzulo, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Cdedi a Silvestre Namiwa ati mkumanowo sudathandize Amalawi pankhani ya njala.

Iwo ati polingalira momwe njala ikukolerera m’dziko muno, bilu ya chimanga ikadakhala koyambirira kuti ikambidwe ndi kutha msanga kuti zina za mubiluyo zothandiza kuchepetsa njala ziyambike.

Anthu 4 miliyoni ali pa chiopsezo cha njala

Mwa zina, iwo adati biluyo ndi yothandiza kuti boma likhoza kupereka makontirakiti olima chimanga cha mthirira ku makampani akuluakulu kuti chizisokelera miyezi ya njala.

“Akadakambirana ndi kuvomereza bilu imeneyi bwenzi pano akukonzekera kuti makontirakiti ayenda bwanji ndiye kuti potengera ndi momwe njala ilili, pofika December bwenzi tikuyembekezera chimanga cha mthirira,” adatero a Namiwa.

Koma iwo ati n’zodandaulitsa kuti ngakhale mabungwe ndi akadaulo adayesetsa kupanga phokoso za biluyo, nyumbayo idasankha kutseka m’makutu mpakana yamaliza mkumano wake.

Mkumanowo uli mkati, aphungu adakwekwesa nduna ya za malimidwe a Sam Kawale kuti alongosole bwino zomwe boma likuchita pofuna kuti njala isapweteke anthu m’dziko muno.

Wapampando wa komiti yoona za malimidwe a Sameer Suleman adachenjeza boma kuti likangowodzera pang’ono ntchito zambiri zidzaima chifukwa boma lidzakhala likulimbana ndi njala.

“Zomwe tikunena nzoti ngati akunena chilungamo kuti chimanga chilipo chokwanira, achimwaze m’misika kuti anthu agule chifukwa komwe tikuloweraku ntchito idzakula mapeto ake zina zidzaima,” adatero a Suleman.

A Kawale adabwereza mawu awo kuti chimanga chilipo koma aphungu adaonetsa kusagwirizana nazo pong’ung’udza iwo akuwerenga sitetimenti yawo m’nyumayo.

“Panopa ku nkhokwe za boma kuli Chimanga chokwana matani 68 420. Matani 52 460 ndi a NFRA pomwe matani 15 960 ndi cha Admarc. Kuonjezera apo, boma ligula chimanga chokwana matani 42 000 ndi K12 biliyoni ya mu bajeti,” adatero a Kawale.

Pa mkumanowo, nyumbayo idavomereza mabilu anayi okhudza ngongole zoti boma libwereke n’kuthandizira kulimbikitsa ntchito za ulimi makamaka wa mthirira.

Ena mwa mabiluwo ndi ngongole zokwana K276 biliyoni zoti boma libwereke ku International Development Association (IDA) ya World Bank ndi International Bank for Reconstruction (IBR) za gawo lachiwiri la pulojekiti ya Agcom.

Nduna ya za chuma a Sosten Gwengwe adati mabiluwo athandiza kulimbikitsa ntchito yothana ndi njala makamaka podzera mu ulimi wa mthirira ndi mapulojekiti ena othandiza anthu kuti azikhala n’chakudya chokwanira.

“Dziko lililonse loganizira za anthu ake limayenera kuonetsetsa kuti pali njira zokhazikika zoti anthu a m’dzikolo azikhala n’chakudya, mabilu amene avomelezedwawa ntchito yake ndi imeneyo ndipo atithandiza kwambiri,” adatero a Gwengwe.

M’mapulani a boma a Malawi 2063, nkhani imodzi yaikulu ndi yolimbikitsa ulimi wamakono monga mthirira, kugwiritsa ntchito makina apamwamba pa ulimi komanso kutsegula misika ya zokolola ya mphamvu.

Malingana ndi a Gwengwe, masomphenya amenewa akhoza kutheka ndi pulojekiti ya Agcom yomwe aphungu pamkumano wapitawu adavomereza ndalama zake za gawo lachiwiri.

Pa mkumanowo nkhani ina yomwe idamanga nthenje idali yokhudza ndalama zomwe anthu amapereka pobwezeretsa ziphaso za unzika, nthawi yomwe ziphaso zimatenga kuti zituluke komanso nkhani yokhudza tsiku lothera mphamvu yachiphaso.

Nduna ya za chitetezo cha m’dziko a Ken Zikhale Ng’oma adalonjeza m’nyumbayo kuti akonza zonsezo ndipo pano nthambi yopanga ziphaso ya NRB yalengeza kuti munthu sazipelekaso ndalama pobwezeretsa zitupa komanso zitupa zonse zizigwira ntchito mpaka pa 1 January 2026.

Related Articles

Back to top button