Nkhani

Atsogoleri akwangula kampeni lero

Listen to this article

Migwirizano ya zipani pachisankho chikudzachi zikuomba mkota wa mfundo za kampeni lero ndipo atsogoleri a m’migwirizanoyo akhala ali mbweee! kutolera mavoti otsalira.

Bungwe la chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) dzulo lidati misonkhano ya kampeni itsekedwa pokwana 6 koloko mawa mmawa.

Mutharika (Kumanzere) ndi Chakwera ndiwo atengetsana kwambiri

Malingana ndi mkulu woyang’anira za kampeni m’chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Moses Kunkuyu, mtsogoleri wa MCP Lazarus Chakwera akhala pabwalo la Masintha ku Lilongwe pomwe othandizana naye mu mgwirizano wa Tonse Saulos Chilima wa UTM akhala ku Blantyre.

“Tikufuna tikumbutse anthu mfundo zathu. Tidadutsamo kale koma tikawakumbutse ndi kuwatsimikizira kuti takonzeka kulowa m’boma,” adatero Kunkuyu.

Koma Lachinayi, Mgeme Kalilani yemwe ndi mneneri wa mtsogoleri wa mgwirizano wa DPP ndi UDF Peter Mutharika adati pulogalamu ya momwe Mutharika akwangulire kampeni yake siyidatsimikizike.

Mutharika akupangira limodzi kampeni ndi Atupele Muluzi wa UDF yemwe ndi wotsagana naye  mumgwirizano wawo.

Panyengoyi, migwirizano ya Tonse Alliance komanso DPP/UDF zalonjeza mfundo zosiyanasiyana zachitukuko komanso umoyo wabwino.

Mwa zina, mgwirizano wa Tonse Alliance udatsindika zotsitsa mtengo wa feteleza kufika pa K4 500 thumba la makilogalamu 50, kulemba ntchito achinyamata omwe ali paulova ngakhale ali ndi zoyenereza, kuthetsa mchitidwe wa tsankho, kuyambitsa ndondomeko yoti anthu okalamba azilandira ndalama pamwezi ndi kutukula ntchito zamalimidwe, zaumoyo ndi kulemekeza malamulo.

Mgwirizano wa DPP/UDF mfundo zake mudali nkhani yolimbikitsa kutukula achinyamata powaphunzitsa ntchito zamanja ndi kuwapatsa ngongole, kutukula amayi pantchito zosiyanasiyana, kulimbikitsa umodzi ndi chilungamo, kutukula ulimi popitiriza pulogalamu ya sabuside, kutukula ntchito za makina a kompyuta pogawa mayuniti a Intaneti aulere komanso kupitiriza pulogalamu yolemba achinyamata ntchito.

Ngakhale kampeni yafika kumapeto chonchi, migwirizanoyi yayenda mowirira makamaka pa nkhani ya zipolowe ndi kuchitirana zamtopola zosiyanasiyana.

Anthu ena kumbali zonse adamenyedwa, kuvulazidwa, kuphwanyiridwa ndi kuotcheredwa katundu chifukwa chopezeka m’madera omwe ena amaona kuti samayenera kupezekako.

Mneneri wapolisi James Kadadzera adatsimikiza kuti apolisi adalandira malipoti oti anthu ena amachitira zamtopola anzawo pakampeni ndipo adalonjeza kuti akufufuza malipotiwo.

Pa zokwangula kampeni lero, Kadadzera wati apolisi ayesetsa kupezeka paliponse makamaka komwe kuchitikire misonkhano kuti pasakhale za mtopola zilizonse.

“Ndi cholinga chathu kuti anthu amvetsetse mfundo zotsiriza. Ukapita mwayi uwu, anthu sadzapezanso mpata omva mfundo za atsogoleri awo pachisankhochi ndiye ndi ntchito yathu kukhazikitsa bata,” adatero Kadadzera.

Zipangizo zovotera pachisankhochi zafika dzulo mu mzinda wa Lilongwe ndipo bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) likhala likutumiza zipangizozo m’maboma.

Related Articles

Back to top button
Translate »