Nkhani

Bambo amwalira pofuna kulemera

Bambo wina m’boma la Dedza wamwalira atamwa mankhwala oti alemere.

“Ukakamwa mankhwalawa, ukafa sabata imodzi. Ukatuluka mphutsi, ndipo  akazi awo akatole mphutsizo zomwe zikasanduke ndalama. Kenaka ukadzukanso.”

Awa ndi mawu amene sing’anga wina m’dziko la Mozambique akuganiziridwa kuti adauza bamboyo, Limbani Nsalawatha kuti akachite.

Izitu zidachitika pa 13 September pamene bamboyu adakagwada kwa sing’anga pofuna kuthana ndi umphwawi.

Malinga ndi mkazi wa bamboyo, Gloria, sing’angayo akuti adapatsa mwamuna wake mankhwala amene adamuchenjeza kuti afa kwa sabata imodzi yokha ndipo akadzuka.

Mayiyu, adauza apolisi ya Dedza kuti mwamuna wake adafadi atangobwera kwa sing’angayo adauzidwa kuti asauze munthu za imfa yake ndipo azidzangotolera mphutsi zake ndikuika m’thumba momwe zidzasanduke ndalama.

“Akuti adamuuza kuti sabata ikangotha, mwamuna wake adzuka ndipo adzakhala akusangalala ndi ndalama zomwe apanga kuthetseratu umphawi wawo,” adatero mneneri wa police ya Dedza Edward Kabango.

“Atafa sadalire kapena kuuza anthu. Mmalo mwake adayika thupi lake m’chipinda chapadera kwa masiku 6,” adaonjeza Kabango.

Gloria akuti adauza apolisiwa kuti nkhani yonse idadziwika pamene anzake oyandikana nyumba adayamba kumva fungo la chinthu choola komanso ntchentche zomwe zimauluka mozinga nyumbayo.

“Pochita mantha iye adathamangira kwa achibale a bamboyo amene adafika pakhomopo. Nkhaniyi idafikira kupolisi ya Njonja isadafike kupolisi kwathu,”  adatero Kabango.

Pa 20 September bamboyu akuti amayembekezera kudzuka malinga ndi zomwe adauzidwa kwa ng’anga koma mkazi wake adangoona chetechete popanda kutakataka mmalo mwake mphutsi ndizo zimasangalala.

Pa 21 malemuwa adakaikidwa mmanda. Zotsatira za chipatala, zidaonetsa kuti Nsalawatha, 22, adamwalira chifukwa chobanika.

Apolisi achenjeza anthu kuti asamangotengeka ndi zilizonse.

“Si zoona kuti mphutsi zingasanduke ndalama. Ili ndi bodza ndipo anthu asatengeke ndi zilizonse,” adalangiza Kabango.

Malemuwa amachokera m’mudzi mwa chimowa kwa T/A Kachere m’boma la Dedza.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button