Nkhani

Boma ligulitsa chimanga pamtengo wa sabuside

Kadaulo pazamalimidwe Tamani Nkhono-Mvula wati boma likhale ndi ndondomeko yokhwima yogulitsira chimanga pa mtengo wa sabuside ngati momwe lakonzera poopa akamberembere.

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adalengeza Lamulungu lapitali kuti boma lake lakonza zogulitsa chimanga kumsika wa Admarc pa mtengo wotsikirako kuti lipulumutse anthu omwe alibe chakudya komanso ndalama zogulira chakudyacho.

Anthu akugula chimanga ku Admarc mmbuyomu

“Ndidakambirana ndi nduna ya zamalimidwe komanso ya zachuma ndipo tidagwirizana kuti panopa chimanga tigulitse pa mtengo wotsikirako kuti anthu asamve kupweteka kwambiri ndi nyengo ya matendayi chifukwa asokoneza ntchito zambiri,” adatero Chakwera.

Koma Nkhono-Mvula wati nthawi zambiri kukakhala chikonzero chotere, mavenda amalowererapo nkugula chimanga chambiri chomwe amadzagulitsanso ku Admarc chikatha kapena kwa anthu pamtengo obowola mthumba.

“Mfundo yanga ndi yoti pakhale ndondomeko yeniyeni ya momwe chikonzerochi chidzayendere apo ayi ganizo labwino ngati ili silidzaoneka phindu lake,” watero Nkhono Mvula.

Iye wati chikonzerochi n’chabwino kwambiri koma zikhoza kukhalanso bwino boma litapeza njira yokhazikika yoti anthu asamakhalenso ndi njala mmalo momadalira njira ya sabuside.

“Chimodzi mwa zifukwa zomwe Admarc idakhazikitsidwira n’kuonetsetsa kuti anthu azipeza chakudya motsika mtengo pakakhala mavuto ngati amenewa a Covid 19 koma sitingamati sabuside pa zipangizo zaulimi kenakonso sabuside pa chakudya ayi. Tikufunika njira yothetseratu njalayo,” watero Nkhono-Mvula.

Mkulu wa bungwe loona za anthu ogula, kudya ndikugwiritsa ntchito katundu la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wati chikonzerochi chabwera nthawi yabwino pomwe anthu ambiri ali mmavuto azachuma chifukwa cha corona.

“Zafika nthawi yoyenera chifukwa anthu ambiri akuoneka kuti asowa chakudya ndipo alibe ndalama zogulira chifukwa mwina adachotsedwa ntchito kaamba ka mayendawa kapena bizinesi zawo sizikuyenda,” watero Kapito.

Dziko la Malawi limadalira chimanga ngati chakudya chenicheni chodalirika ndipo alimi ambiri amalima chimanga chakudya komanso chogulitsa.

Zaka zapitazi ntchito ya Admarc idalowa pansi moti anthu amadalira misika ya mavenda akafuna chimanga zomwe zimapangitsa kuti mitengo ya chimanga izikwera kwambiri m’madera ena.

Boma lidapanganso dongosolo yoti bajeti yaboma iziyamba pa 1 April chaka chilichonse kuti mabungwe ngati Admarc azilandira msanga ndalama zogulira chimanga ndi mbewu zina mavenda asadasese nkhokwe za alimi.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button