Nkhani

Boma lithetsa mafumu m’mizinda

Listen to this article

 

Zavuta kumpando. Kalata ya boma yothetsa mafumu amene amalamulira m’mizinda ya Blantyre, Zomba, Lilongwe, Mzuzu komanso Luchenza yaika pampanipani mafumuwa ndipo akagwada kuboma kuti liganizenso kachiwiri pankhaniyi.

Pa 21 May 2015, unduna wa maboma aang’ono udatulutsa kalatayi m’mene mwa zina idati kuyambira tsopano mafumuwa sazilandiranso malipiro awo apamwezi (mswahara).

Njambe (L) ndi Chiwembe amene adali nawo m’gulu la mafumu amene adakapereka kalata yodandaula kwa DC
Njambe (L) ndi Chiwembe amene adali nawo m’gulu la mafumu amene adakapereka kalata yodandaula kwa DC

Izi zatsutsula mafumuwa, amene m’sabatayi adakapereka madandaulo awo kwa ma DC a mizinda yokhudzidwayo kuti ganizoli lisinthidwe. Mafumu amene akhudzidwawa ndi nyakwawa (village headmen), gulupu (group village headmen) komanso ma Sub T/A.

Koma mlembi muundunawu Lawrence Makonokaya, wati ngakhale mafumuwa akulira chonchi, unduna wawo ulibe maganizo osintha mfundoyi.

“Tidayamba kalekale kuwakumbutsa kuti ufumu wawo ndi wosaloledwa pamalamulo okamba za ufumu (Chiefs Act) koma iwo ankazengereza. Apa palibe kukambirana, ufumu wawo watha chifukwa udali wosaloledwa,” adatemetsa nkhwangwa pamwala Makonokaya.

Gawo lachiwiri, ndime ya chisanu m’malamulo okhudza mafumu la Chiefs Act, limanena kuti sipadzakhala Paramount Chief, Senior Chief, Chief kapena Sub-Chief amene adzagwire ntchito mumzinda kapena m’tauni pokhapokha patakhala chilolezo chochokera kukhonsolo ya mzindawo, yomwe idzalumikizane ndi unduna wa maboma aang’ono popereka chilolezocho.

Izi zikusonyeza kuti mafumuwa alibe mphamvu zomalamula m’mizindayi monga zakhala zikuchitikira mmbuyomu, zomwe zadzidzimutsa atsogoleriwa, amene akhala akulamula komanso kumalandira mswahara.

Kaamba ka kuwawidwa, mafumu ena mumzinda wa Blantyre, Lolemba adakumana kwa Manje mumzindawu pamene adayenda ulendo wandawala kukapereka chikalata kwa DC wawo, Charles Kalemba.

Iwo adati ufumu si ntchito yoti adachita kufunsira polemba kalata koma adachita kubadwa nawo kotero boma lalakwitsa kuwachotsa.

Gulupu Njambe, yemwe adayenda nawo, adati sangalankhule zambiri kwa atolankhani popeza nkhaniyi ili mkati kukambidwa.

“Koma tikufunani atolankhani posakhalitsapa pazomwe zachitikazi. Ife mafumu ndife owawidwa kwambiri,” adatero movomerezana ndi nyakwawa Chiwembe.

Senior Chief Kapeni wa m’boma la Blantyre wati nkhaniyi ndi yachisoni kotero akuyesera kuti akambirane ndi boma.

“Mafumu anga ndi okhumudwa, ndisakunamizeni. Nkhaniyi ndi yachisoni. Ndidawaitanitsa mafumu onse ndipo akhumudwa pomva nkhaniyi. Komabe tikuyembekezera kuti boma lisintha ganizoli chifukwa tikhala ndi zokambirana posakhalitsapa,” adatero Kapeni.

Nako ku Zomba mafumu akuti adachita thukuta ndi nkhaniyi ndipo adapita kwa DC wawo kuti awafotokozere bwino chomwe kalatayo imatanthauza.

T/A Mlumbe adauza Tamvani kuti, “padali kusamvetsetsana pa chomwe kalatayo imatanthauza ndipo takatula nkhawa zathu kwa DC. Koma ndinene pano kuti mafumu ena salola. Ndili ndi mafumu 600 ndipo ena akhudzidwa nawo.”

Ku Mzuzu ndi ku Lilongwe mafumu kumenekonso adakadandaula za nkhaniyi kwa ma DC awo.

Koma mphunzitsi wa zandale ku sukulu ya Chancellor College Blessings Chinsinga akuikira kumbuyo ganizo la boma.

“Zilibwino kwambiri. Dziwani kuti ntchito za mafumuwa zimaoneka chifukwa tidalibe makhansala, lero tasankha makhansala ndiye tikhalenso ndi mafumu?” adatero Chinsinga.

“Ngakhale ndikuyamika boma kuti lachita chabwino, mbali imeneyi aisamalitse kuti pasakhalenso mberewere ndi kuchoka kwa mafumu m’mizinda chifuwa ena atha kunena kuti asiya ufumuwo koma akugwirabe mobisalira,” adatero Chinsinga.

Ntchito zina zomwe mafumuwa amagwira ndi monga kutsogolera ntchito zachitukuko m’madera; kuyang’anira manda; komanso kuyendetsa zitukuko zomwe zabwera ndi boma komanso mabungwe monga ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo, ndondomeko ya LDF ndi zina.

Koma Makonokaya akuti iye sangalankhulepo kuti ntchitozi zizikhala bwanji chifukwa amene akuyenera kudziwa momwe zizikhalira ndi amene akuyang’anira mizinda.

Malinga ndi unduna wa maboma aang’ono, m’dziko muno muli mafumu 42 079. Mwa mafumuwa, 7 ndi ma Paramount Chief, 39 ndi ma Senior Chief, 164 ndi ma T/A pamene 59 ndi ma Sub T/A. Magulupu alipo 7 492 pamene 34 589 ndi nyakwawa.

Malinga ndi mneneri muunduna wa maboma ang’ono Muhlabase Mughogho, mafumu 298 ndiwo akhudzidwe ndi chigamulochi.

Related Articles

Back to top button