Chichewa

Bullets, manoma akunthana lero

Listen to this article
Kumakhala fumbi nthawi zonse Bullets (zifiira) ndi Wanderers akamakumana
Kumakhala fumbi nthawi zonse Bullets (zifiira) ndi Wanderers akamakumana

Tsoka mtunda ndi nyanja popeza woipayo watsikira pa Civo Stadium masanawa. Ligi ya TNM Super League tsopano yafika pa gwiritse.

Nkhawa ili biii! Kwa osapotera timu ya Big Bullets ndi Mighty Wanderers pamene matimuwa akhale akuphananso masanawa.

Iyi ikhala nkhondo yeniyeni chifukwa ngati Nyerere zipambane masewero asanu amene yatsala nawo ndiye kuti zikhala ndi mapointsi 55 kutanthauza kuti iposa matimu onse. Apa ndiye kuti zili ndi mwayi wophulanso ligiyi patangodutsa mwezi zitanyamula chikho cha Standard Bank.

Koma mwina loto la Wanderers lingakhale lovuta chifukwa mphunzitsi watsopano wa Bullets, Gerald Phiri, akuti akulotanso atapambana masewero asanu amene timuyi yatsala nawo kuti mwina angathere pabwino kapena kutenga ligi.

Bullets ikuchokera kolepherana mphamvu ndi Blantyre United. Iyo ili pa nambala 6 ndi mapointsi 36. Pamene Nyerere zikuchokera koboola jombo ya Moyale ku Balaka ndi zigoli ziwiri kwa duuu! Izo zili pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 40 kutsogozedwa ndi Red Lions yomwe ili ndi mapointsi 41 koma yatsala ndi magemu anayi.

Masewero a Wanderers ndi Bullets ali pa Civo pamene pakhale pakhomo pa Nyerere. Timuyi ndiyo yasankha bwaloli chifukwa pa Kamuzu idathamangitsidwa patachitika ziwawa ndipo siidamalize chilango.

Koma mlembi wa Nyerere David Kanyenda akukhulupirira kuti lero Maule aona mbonaona.

“Mukaonetsetsa takhala tikuchita bwino, sitikuchinyitsa zigoli. Tikuchokera kopambana ndi Moyale, ndipo dziwani kuti Bullets ndi akazi athu,” akutero Kanyenda.

Matimuwa akumanapo kawiri posakhalitsapa. M’ndime yoyamba ya ligiyi, matimuwa adalepherana mphamvu pochinyana chigoli chimodzi kwa chimodzi.

Matimuwa adakumananso ku Lilongwe mubonanza ya Luso TV pomwe Bullets idapambana kudzera m’mapenote.

Matimu ena akhalenso akuphana m’chikhochi masanawa. Mzuzu United ikhomana ndi Civo United pa Mzuzu Stadium. Evirom ithyolana ndi Blue Eagles pa   Kamuzu. Jombo ya Red Lions ili pakhomo ndi Kamuzu Barracks ku Zomba.

Mawa, Blantyre United iphwanyana ndi Blue Eagles pa Kalulu Stadium. Epac F.C ikwapulana ndi Silver Strikers pa Civo Stadium. Moyale ikumana ndi Civo United   pa Mzuzu Stadium. Azam Tigers igogodana ndi Kamuzu Barracks         ku Balaka Stadium. Evirom ikumananso ndi Mafco FC pa Kamuzu Stadium.

Related Articles

Back to top button
Translate »