Nkhani

Chimanga ‘amachibisa’ chatuluka

Patangotha masiku ochepa boma litayamba kulandira chimanga chomwe lagula m’dziko la Zambia, mavenda nawo atulutsa chimanga chawo chomwe akufuna kukagulitsa ku misika ya Admarc ndi nkhokwe za boma za NFRA.

Izi zautsa manong’onong’o woti mavenda ena amabisa dala chimangacho poyesa kuti chidzakwera mtengo ndipo adzapange ndalama zambiri pogulitsa.

Malingana ndi nduna ya za malimidwe Mayi Roza Mbirizi, mavenda adagula chimanga chambiri ndipo mmalo mochigulitsa, ankangochisunga pomwe anthu amalira ndi njala.

“Chimanga chidalipo ndipo umboni wake waoneka pomwe galimoto za mtengatenga zandanda m’misewu kufuna kukagulitsa chimanga. Kumeneku n’kusokoneza mapulani aboma,” atero a Mbirizi.

Kuyenda m’misewu ina mu mzinda wa Lilongwe kukuvuta kaamba koti galimotozo zayalana kulowera ku misika ya Admarc.

Mkulu wa bungwe la Malawi Agricultural Policy Advancement and Transformation Agenda (Mwapata) Institute a William Chadza ati mpofunika kuti boma lizikhala ndi njira zoti chimanga chisamasowe pa msika.

Iwo ati n’zodabwitsa kuti pompano mbiri idali yoti chimanga kulibe koma chitangoyamba kufika chochokera ku Zambia, amalonda a m’Malawi nawo akhamukira ku msika.

“Apapa zikuonetsa kuti pali kagulu kena kake komwe kamati alimi akamakolola kamagula chimanga limodzi ndi mbewu zina n’kubisa. Koma zimenezi n’zofunika njira yozithetsera,” atero a Chadza.

Boma lidagula matani 200 000 m’dziko la Zambia kuti lisokelele pomwe pamaperewera malipoti atasonyeza kuti anthu oposa 4 miliyoni asowa chakudya pakati pa miyezi ya November 2025 ndi April 2026.

A NFRA atalengeza kuti ayamba kugula chimanga pa mtengo wa K55 000 pa thumba la makilogalamu 50, mavenda ambiri akuthamangira kokagulitsa kuopa kuti mtengowo ungagwenso.

Wogwirizira mpando wa za kafukufuku ku bungwe la National Planning Commission (NPC) a Andrew Jamali adati mpofunika kukhala ndi njira yolondolozera zokolola ndi momwe zikugwira ntchito.

“Ngati dziko tikuyenera kumadziwa kuti zokolola zathu zikuyenda bwanji chifukwa tikhonza kumangodandaula chonsecho tili ndi zokwanira. Komanso boma lizitha kuteteza chimanga kuti chisamatuluke wamba,” atero a Jamali.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button