Nkhani

chiwanda chophana chavuta

Listen to this article

Chiwanda chachilendo chophana m’mabanja chalowerera moti mwezi umodzi okha, bambo wina ku Zomba adapha mkazi wake, banja lina ku Chiradzulu lidapha mwana wawo pomwe mwana wa zaka 15 ku Chitipa adapha agogo ake.

Lachitatu pa 10 October 2023 bambo wa zaka 27 a Dube Nkhwinjiri adapha mkazi wawo wa zaka 20 Ndiuzayani Pemphani m’boma la Zomba pa nkhani yokhudzana ndi masilamusi omwe bamboyo ankafuna kuchita.

Mneneri wapolisi m’boma la Zomba mayi Patricia Sipiriyano atsimikiza kuti akusunga m’chitokosi bamboyo yemwe kafukufuku akatha akayankhe mlandu wakupha.

“Tidalandira lipoti loti bamboyo yemwe amakhala m’mudzi mwa Muwa kwa Jali wapha mkazi wake ndipo titapita m’mudzimo tidapezadi kuti mkaziyo ali thapsya m’magazi ake omwe atabaidwabaidwa,” atero a Sipiriyano.

Koma munthu yemwe adatitsina khutu za nkhaniyi adati bamboyo adakatenga mankhwala woti alemere ndipo adauzidwa kuti akakwirire mankhwalawo m’nyumba kuti aphe mwana wake akhwimire.

“Atachita izi, mwana wakeyo atalowa m’nyumbamo adakomoka koma mwachangu mkazi wake adakafukula mankhwalawo mwanayo n’kutsitsimuka ndipo pomwepo bamboyo adachita misala,” adatero iwo.

A Sipiriyano adatsimikiza zoti bamboyo adachita misala sabata ziwiri zapitazo koma adakachira ku mapemphero n’kubwerera ku mudzi komwe atangofika adapha mkazi wakeyo.

“Lipoti lomwe talandira ndi loti atachila n’kubwerera ku mudzi pa 10 October, anthu adadabwa kumuona atatenga ana ake awiri n’kulowera nawo kwa agogo awo modabwitsa ndipo anthuwo atathamangira ku nyumba kwake adakapeza mkazi wake atagona m’magazi,” adatero a Sipiriyano.

Iwo ati bamboyo ndi malemu mkazi wakeyo onse amachokera m’mudzi mwa Mutheko kwa mfumu yayikulu Mwambo m’boma la Zomba.

Nako ku Chiradzulu banja lina lili m’manja mwa apolisi powaganizira kuti adapha mwana wawo wa miyezi 5 chifukwa bambo wa m’nyumbamo a Robert Miliyasi a zaka 27 amakaika kuti mwanayo ndi wawo.

Mneneri wa polisi ya Chiradzulu a Cosmas Kagulo ati banjalo lidayamba m’chaka cha 2018 mkaziyo ali kale ndi ana awiri ndipo akhala akulekana n’kubwererananso katatu konse.

Iwo ati ulendo womaliza, mkaziyo Regina Tomasi wa zaka 22 adali ndi pakati koma bamboyo ankakaika kuti mimbayo idali yake mpakana adasiyananso mkaziyo n’kubwerera kwawo.

“Kafukufuku wathu wapeza kuti mwana atabadwa mwezi wa May 2023, mayiyo adapereka maganizo woti angomupha kuti asasokoneze banjalo ndipo adayesa kawiri konse kuti aphe mwanayo koma zimavuta.

“Pa 4 October 2023 mkazi uja adazondotsera mwanayo m’ndowa yodzadza ndi madzi mpaka adafa kenako adamubereka ngati ali moyo n’kupita naye kwa makolo ake komwe abale ake adazindikira kuti mwanayo n’chitanda,” atero a Kagulo.

Iwo ati abalewo atapanikiza mayiyo ndi mwamuna wake adavomera kuti adapha mwanayo ndipo nkhani idanka kwa amfumu omwe adaipititsa ku polisi.

Pano banjalo lomwe limachokera m’mudzi mwa Misomali kwa mfumu yaikulu Nkalo lili m’manja mwa apolisi ndipo likuyembekezera kukayankha mlandu wakupha.

Ndipo ku Chitipa mnyamata wa zaka 15 akumuganizira kuti adapha agogo ake powasinga khosi ndi chikwakwa powaganizira kuti adapha abambo ake m’matsenga.

Mneneri wapolisi ku Chitipa a Gladwell Simwaka atsimikiza koma pomwe timalemba nkhaniyi nkuti asadatitumizire nkhani yonse momwe idakhalira kuti zifike poti mwanayo aphe agogowo.

Related Articles

Back to top button
Translate »